LEVITIKO 24 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Za mafuta a nyalizo ndi mkate woonekera(Eks. 27.20-21)

1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2Uza ana a Israele, kuti akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti aziwalitsa nyali nthawi zonse.

3Aroni aikonze kunja kwa nsalu yotchinga ya mboni, m'chihema chokomanako, kuyambira madzulo kufikira m'mawa, pamaso pa Yehova nthawi zonse; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu.

4Akonze nyalizo pa choikaponyali choona pamaso pa Yehova nthawi zonse.

5Ndipo uzitenga ufa wosalala, ndi kuphika timitanda khumi ndi tiwiri; awiri a magawo khumi a efa afikane kamtanda kamodzi.

6Ndipo utiike m'mizere iwiri, tisanu ndi kamodzi mzere umodzi, pa gome loyera, pamaso pa Yehova.

7Nuike lubani loona ku mzere uliwonse, kuti likhale kumkate ngati chokumbutsa, nsembe yamoto ya Yehova.

8Nthawi zonse tsiku la Sabata aukonze pamaso pa Yehova, chifukwa cha ana a Israele, ndilo pangano losatha.

91Sam. 21.6Ndipo ukhale wa Aroni ndi ana ake, audye pamalo popatulika; pakuti auyese wopatulika kwambiri wochokera ku nsembe zamoto za Yehova; ndilo lemba losatha.

Kulangidwa kwa wotemberera Mulungu ndi ochimwira zina

10Ndipo mwana wamwamuna wa mkazi Wachiisraele, atate wake ndiye Mwejipito, anatuluka mwa ana a Israele; ndi mwana wamwamuna wa mkazi Wachiisraeleyo analimbana naye munthu Mwisraele kuchigono;

11Eks. 20.7; Afi. 2.9-10ndipo mwana wamwamuna wa mkazi Wachiisraele anachitira Dzina mwano, natemberera; ndipo anadza naye kwa Mose. Dzina la mai wake ndiye Selomiti, mwana wa Dibiri, wa fuko la Dani.

12Ndipo anamsunga m'kaidi, kuti awafotokozere m'mene anenere Yehova.

13Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

14Tuluka naye wotembererayo kunja kwa chigono; ndipo onse adamumva aike manja ao pamutu pake, ndi khamu lonse limponye miyala afe.

15Ndipo unene ndi ana a Israele, ndi kuti, Aliyense wotemberera Mulungu wake azisenza kuchimwa kwake.

16Lev. 24.11Ndi iye wakuchitira mwano dzina la Yehova, amuphe ndithu; khamu lonse limponye miyala ndithu; mlendo ndi wobadwa m'dziko yemwe akachitira dzina la Yehova mwano, awaphe.

17Eks. 21.12Munthu akakantha munthu mnzake aliyense kuti afe, amuphe ndithu.

18Munthu akakantha nyama kuti ife, ambwezere ina; moyo kulipa moyo.

19Mat. 5.38Munthu akachititsa mnansi wake chilema, monga umo anachitira momwemo amchitire iye;

20kuthyola kulipa kuthyola, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino; monga umo anachitira munthu chilema, momwemo amchitire iye.

21Iye wakukantha nyama kuti ife, ambwezere ina; iye wakupha munthu, amuphe.

22Chiweruzo chanu chifanefane ndi mlendo ndi wobadwa m'dziko; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

23Ndipo Mose ananena ndi ana a Israele, ndipo anatulutsa wotembererayo kunja kwa chigono, namponya miyala. Ndipo ana a Israele anachita monga Yehova adauza Mose.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help