AEFESO 5 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 Mat. 5.45, 48 Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa;

2Yoh. 13.34; 2Ako. 2.15; Agal. 2.20ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.

3Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima;

4Aef. 4.29kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko.

5Agal. 5.19-21Pakuti ichi muchidziwe kuti wadama yense, kapena wachidetso, kapena wosirira, amene apembedza mafano, alibe cholowa mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu.

6Mat. 24.4Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda pake, pakuti chifukwa cha izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.

7Chifukwa chake musakhale olandirana nao;

8Yoh. 8.12; 12.36, 46pakuti kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika,

9pakuti chipatso cha kuunika tichipeza mu ubwino wonse, ndi chilungamo, ndi choonadi,

10kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani;

111Ako. 5.9, 11; 10.20ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse;

12Aro. 1.24, 26pakuti zochitidwa nao m'tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi.

13Yoh. 3.20-21Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera; pakuti chonse chakuonetsa chili kuunika.

14Yes. 60.1; Aro. 6.4-5; 13.11-12Mwa ichi anena, Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe.

15 Akol. 4.5 Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru;

16akuchita machawi, popeza masiku ali oipa.

171Ate. 4.3Chifukwa chake musakhale opusa, koma dziwitsani chifuniro cha Ambuye nchiyani.

18Miy. 20.1; Luk. 21.34Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu,

19Mac. 16.25ndi kudzilankhulira nokha ndi masalimo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu;

20Mas. 34.1; Akol. 3.17ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, chifukwa cha zonse, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu;

21Afi. 2.3ndi kumverana wina ndi mnzake m'kuopa Khristu.

Zoyenera m'banja la munthu

22 Akol. 3.18 Akazi inu, mverani amuna anu a inu eni, monga kumvera Ambuye.

231Ako. 11.3Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Khristu ndiye mutu wa Mpingo, ali yekha Mpulumutsi wa thupilo.

24Komatu monga Mpingo amvera Khristu, koteronso akazi amvere amuna ao m'zinthu zonse.

25Akol. 3.19Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Khristu anakonda Mpingo, nadzipereka yekha m'malo mwake;

26Tit. 3.5kuti akampatule, atamyeretsa ndi kumsambitsa madzi ndi mau;

272Ako. 11.2kuti Iye akadziikire yekha Mpingo wa ulemerero, wopanda banga, kapena khwinya, kapena kanthu kotere; komatu kuti akhale woyera, ndi wopanda chilema.

28Koteronso amuna azikonda akazi ao a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha;

29pakuti munthu sanadane nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga, monganso Khristu Mpingo;

30Aro. 12.5pakuti tili ziwalo za thupi lake.

31Gen. 2.24; Mrk. 10.7-8Chifukwa cha ichi munthu azisiya atate ndi amai, nadzaphatikizana ndi mkazi wake; ndipo iwo awiri adzakhala thupi limodzi.

32Chinsinsi ichi nchachikulu; koma ndinena ine za Khristu ndi Mpingo.

331Pet. 3.6Komanso inu, yense pa yekha, yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo akumbukire kuti aziopa mwamuna.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help