EZEKIELE 27 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Nyimbo ya maliro ya pa Tiro

1Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,

2Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, Takwezera Tiro nyimbo ya maliro;

3Ezk. 28.2nuti kwa Tiro, Iwe wakukhala polowera m'nyanja, wakuchita malonda ndi mitundu ya anthu m'zisumbu zambiri, atero Ambuye Yehova, Iwe, Tiro, wati, Ine ndine wokongola wangwiro.

4M'mphepete mwako muli m'kati mwa nyanja, iwo anakumanga iwe anakonza kukongola kwako kukhale kwangwiro.

5Anacheka matabwa ako onse amlombwa wa ku Seniri, anatenga mikungudza ya ku Lebanoni kukupangira milongoti.

6Anasema nkhafi zako za thundu wa ku Basani, anapanga mipando yako yamnyanga, woika mu mtengo wanaphini wochokera ku zisumbu za Kitimu.

7Thanga lako ndi labafuta wopikapika wa ku Ejipito, likhale ngati mbendera yako; chophimba chako ndicho nsalu yamadzi ndi yofiirira zochokera ku zisumbu za Elisa.

8Okhala mu Sidoni ndi Arivadi ndiwo opalasa ako; anzeru ako, Tiro, okhala mwa iwe, ndiwo oongolera ako.

9Akulu a ku Gebala ndi eni luso ake anali mwa iwe kukonza ziboo zako; zombo zonse za kunyanja pamodzi ndi amalinyero ao anali mwa iwe kusinthana nawe malonda.

10Yer. 46.9Apersiya, Aludi, Aputi, anali m'khamu lako; anthu ako a nkhondo anapachika chikopa ndi chisoti mwa iwe, anamveketsa kukoma kwako.

11Anthu a Arivadi pamodzi ndi ankhondo ako anali pa malinga ako pozungulira, ndi Agamadi anali mu nsanja zako; anapachika zikopa zao pa makoma ako pozungulira, anakwaniritsa kukoma kwako.

122Mbi. 20.36Tarisisi anagulana nawe malonda m'kuchuluka kwa chuma chilichonse; anagula malonda ako ndi siliva ndi chitsulo, seta ndi ntovu.

13Gen. 10.2-7Yavani, Tubala, Meseki, anagulana nawe malonda; ndi anthu amoyo ndi zotengera zamkuwa anagulana nawe malonda.

14Iwo a nyumba ya Togarima anagula malonda ako ndi akavalo, ndi akavalo a nkhondo, ndi nyuru.

15Gen. 10.2-7Anthu a ku Dedani anakutsatsa malonda, zisumbu zambiri zinazolowerana nawe malonda ako, anabwera nazo minyanga ndi phingo kugulana nawe malonda.

16Aramu anachita nawe malonda chifukwa cha zambirizo udazipanga, anagula malonda ako ndi smaragido, nsalu yofiirira, ndi yopikapika, ndi bafuta, ndi korale, ndi ngale.

171Maf. 5.1, 9, 11Yuda ndi dziko la Israele anagulana nawe malonda, anagula malonda ako ndi tirigu wa ku Miniti, ndi zozuna, ndi uchi, ndi mafuta, ndi mafuta amankhwala.

18Damasiko anagulana nawe malonda chifukwa cha zambirizo udazipanga, chifukwa cha kuchuluka kwa chuma chilichonse, ndi vinyo wa ku Heliboni, ndi ubweya wa nkhosa woyera.

19Gen. 10.2-7Vedani ndi Yavani anagula malonda ako ndi thonje, unagulana nao chitsulo chosalala, ngaho, ndi nzimbe.

20Gen. 10.2-7Dedani anagulana nawe malonda ndi nsalu za mtengo wake zoyenda nazo pa kavalo.

21Yes. 60.7Arabiya ndi akalonga onse a ku Kedara anazolowerana nao malonda ako; anaankhosa, nkhosa zamphongo, ndi mbuzi, izi anagulana nawe.

221Maf. 10.1-2; Mas. 72.10, 15Amalonda a ku Sheba ndi a ku Raama anagulana nawe malonda; anagula malonda ako ndi zonunkhira zoposa zilizonse, ndi miyala iliyonse ya mtengo wake, ndi golide.

23Gen. 11.31Harani ndi Kane ndi Edeni, amalonda a ku Sheba Asiriya ndi Kilimadi, anagulana nawe malonda.

24Awa anagulana nawe malonda ndi zovala zosankhika, ndi matumba a nsalu zofiirira ndi zopikapika, ndi chuma cha thonje lopotapota, ndi zingwe zopota zolimba za malonda ako.

25Mas. 48.7Zombo za ku Tarisisi ndizo amtengatenga a malonda ako; ndipo unadzadzidwa ndi chuma ndi ulemu waukulu pakati pa nyanja.

26Opalasa ako anakufikitsa kumadzi aakulu; mphepo ya kum'mawa inakuthyola m'kati mwa nyanja.

27Miy. 11.4; Ezk. 27.34Chuma chako, zako zogulana nazo malonda ako, amalinyero ako, ndi oongolera ako, amisiri ako, ndi ogulitsa malonda ako, ndi ankhondo ako onse okhala mwa iwe, pamodzi ndi msonkhano wonse uli pakati pa iwe, adzagwa m'kati mwa nyanja tsiku la kugwa kwako.

28Ezk. 26.15, 18Pakumveka mfuu wa oongolera ako mabwalo ako adzagwedezeka.

29Ndi onse ogwira nkhafi, amalinyero, ndi oongolera onse a kunyanja, adzatsika kuzombo zao, nadzaima pamtunda,

30Yob. 2.12; Est. 4.1nadzamveketsa mau ao pa iwe, nadzalira mowawa mtima, nadzathira fumbi pamitu pao, nadzakunkhulira m'maphulusa,

31Mik. 1.16nadzameta mpala chifukwa cha iwe, nadzadzimangira ziguduli m'chuuno, nadzakulirira ndi mtima wowawa maliro owawa.

32Chiv. 18.18Ndipo pakulira adzakukwezera nyimbo ya maliro, ndi kukulirira, ndi kuti, Wakunga Tiro ndani, wakunga uyu waonongeka pakati pa nyanja?

33Chiv. 18.19Pakutuluka malonda ako m'nyanja unadzaza mitundu yambiri ya anthu, unalemeretsa mafumu a padziko lapansi ndi chuma chako chochuluka ndi malonda ako.

34Ezk. 26.19Muja unathyoka ndi nyanja m'madzi akuya malonda ako ndi msonkhano wako wonse adagwa pakati pako.

35Ezk. 26.15-16Onse okhala pa zisumbu adagwa nawe, ndi mafumu ao aopsedwa kwambiri, zikhululuka nkhope zao.

36Ezk. 26.21Amalonda mwa mitundu ya anthu akunyodola, wakhala choopsetsa iwe, ndipo sudzakhalanso konse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help