YESAYA 36 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Nkhondo ya Senakeribu idzera Yerusalemu(2Maf. 18.13-27; 2Mbi. 32.1-19)

1 2Maf. 18.13-37 Koma panali chaka chakhumi ndi chinai cha mfumu Hezekiya, Senakeribu, mfumu ya Asiriya anadza, nathira nkhondo pa mizinda ya malinga yonse ya Yuda, nailanda.

2Ndipo mfumu ya Asiriya inatumiza kazembe kuchokera pa Lakisi, kunka ku Yerusalemu, kwa mfumu Hezekiya, ndi nkhondo yambiri. Ndipo iye anaima chifupi ndi mcherenje wa thamanda la kumtunda, m'khwalala la pa mwaniko wa wotsuka nsalu.

3Ndipo anamtulukira Eliyakimu, mwana wa Hilikiya, amene anali wapa nyumba, ndi Sebina, mlembi, ndi Yowa, mwana wa Asafu, mkumbutsi.

4Ndipo kazembeyo anati kwa iwo, Nenani inu tsopano kwa Hezekiya, Itero mfumu yaikulu, mfumu ya Asiriya, Kodi chikhulupiriro ichi nchotani, uchikhulupirira iwe?

5Ine nditi, Uphungu wako, ndi mphamvu zako za kunkhondo, zingokhala mau achabe; tsopano ukhulupirira yani, kuti wandipandukira ine?

6Ezk. 29.6, 9Taona, ukhulupirira ndodo yabango iyi yophwanyika, kunena Ejipito; imene munthu akaitsamira, idzalowa m'dzanja mwake, ndi kulipyoza; momwemo Farao, mfumu ya Aejipito, kwa onse amene amkhulupirira iye.

7Koma ukanena kwa ine, Ife tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; kodi si ndiye amene Hezekiya wachotsa misanje yake ndi maguwa ake a nsembe, nati kwa Yuda, ndi kwa Yerusalemu, Inu mudzapembedzera patsogolo pa guwa la nsembe ili?

8Chifukwa chake upereketu zikole kwa mbuyanga, mfumu ya Asiriya, ndipo ine ndidzakupatsa iwe akavalo zikwi ziwiri, ngati iwe udzaona okwerapo.

9Bwanji tsono iwe ungathe kubweza nkhope ya nduna mmodzi wamng'ono wa atumiki a mbuyanga, ndi kukhulupirira Ejipito, kuti adzakupatsa magaleta ndi apakavalo?

10Ndipo ine tsopano, kodi ndafika opanda Yehova kudzamenyana ndi dziko ili, kudzalipasula? Yehova anati kwa ine, Kwera, ndi kumenyana ndi dziko ili, ndi kulipasula.

11Ndipo Eliyakimu, ndi Sebina, ndi Yowa, anati kwa kazembeyo, Nenanitu kwa atumiki anu m'chinenero cha Aramu; pakuti ife tichimva; ndipo musanene kwa ife mu Chiyuda, m'makutu a anthu amene ali palinga.

12Koma kazembeyo anati, Kodi mbuyanga ananditumiza ine kwa mbuyako ndi kwa iwe kunena mau amenewa? Kodi iye sananditumize ine kwa amuna okhala palinga, kuti adye ndowe zaozao, ndi kumwa madzi aoao ndi inu?

13Pamenepo kazembeyo anaima, nafuula ndi mau aakulu mu Chiyuda, nati, Imvani, inu, mau a mfumu yaikulu, mfumu ya Asiriya.

14Mfumu itere, Musaleke Hezekiya anyenge inu; pakuti iye sadzathai kukupulumutsani:

15ngakhale musaleke Hezekiya akhulupiritse inu kwa Yehova, ndi kunena, Yehova adzatipulumutsa ndithu; mzinda uwu sudzaperekedwa m'manja mwa mfumu ya Asiriya.

16Musamvere Hezekiya, pakuti mfumu ya ku Asiriya itere, Mupangane nane, tulukirani kwa ine; ndipo yense adye mphesa zake, ndi nkhuyu zake, namwe yense madzi a pa chitsime chake;

17Kufikira ine ndidzadza, ndi kunka nanu kudziko lofanana ndi lanu, dziko la tirigu ndi vinyo, dziko la chakudya ndi minda yampesa.

18Chenjerani angakukopeni inu Hezekiya, ndi kuti, Yehova adzatipulumutsa ife. Kodi milungu iliyonse ya amitundu inapulumutsa dziko lao m'manja mwa mfumu ya ku Asiriya?

19Ili kuti milungu ya Hamati, ndi Aripadi? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu? Kodi inapulumutsa Samariya m'manja mwanga?

20Mwa milungu yonse ya maiko awa, inapulumutsa dziko lao m'manja mwanga ndi iti, kuti Yehova adzapulumutsa Yerusalemu m'manja mwanga?

21Koma iwo anakhala chete, osamuyankha mau, pakuti mfumu inawalamulira kuti, Musamuyankhe.

22Ndipo anafika Eliyakimu, mwana wa Hilikiya, amene anali wapa nyumba, ndi Sebina, mlembi, ndi Yowa, mwana wa Asafu, mkumbutsi, kwa Hezekiya ndi zovala zao zong'ambika, namuuza iye mau a kazembeyo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help