MASALIMO 25 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Davide apempha Mulungu amlanditse kwa adaniSalimo la Davide.

1 Mali. 3.41 Ndikweza moyo wanga kwa Inu, Yehova.

2 Mas. 22.5 Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu,

ndisachite manyazi;

adani anga asandiseke ine.

3 Yes. 49.23 Inde, onse akuyembekezera Inu sadzachita manyazi;

adzachita manyazi iwo amene achita monyenga kopanda chifukwa.

4 Eks. 33.13 Mundidziwitse njira zanu,

Yehova; Mundiphunzitse mayendedwe anu.

5Munditsogolere m'choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse;

pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa;

Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.

6 Mas. 103.17 Kumbukirani, Yehova, nsoni zanu ndi chifundo chanu;

pakuti izi nza kale lonse.

7 Yob. 13.26; Yer. 3.25 Musakumbukire zolakwa za ubwana wanga

kapena zopikisana nanu.

Mundikumbukire monga mwa chifundo chanu,

chifukwa cha ubwino wanu, Yehova.

8 Mas. 32.8 Yehova ndiye wabwino ndi wolunjika mtima,

chifukwa chake adzaphunzitsa olakwa za njira.

9Adzawatsogolera ofatsa m'chiweruzo;

ndipo adzaphunzitsa ofatsa njira yake.

10Mayendedwe onse a Yehova ndiwo chifundo ndi choonadi,

kwa iwo akusunga pangano lake ndi mboni zake.

11 Mas. 79.9 Chifukwa cha dzina lanu, Yehova,

ndikhululukireni kusakaza kwanga, pakuti ndiko kwakukulu.

12 Mas. 32.8 Munthuyo wakuopa Yehova ndani?

Adzamlangiza iye njira adzasankheyo.

13 Miy. 19.23 Moyo wake udzakhala mokoma;

ndi mbumba zake zidzalandira dziko lapansi.

14 Miy. 3.32 Chinsinsi cha Yehova chili kwa iwo akumuopa Iye;

ndipo adzawadziwitsa pangano lake.

15 Mas. 141.8 Maso anga alinga kwa Yehova kosaleka;

pakuti Iye adzaonjola mapazi anga mu ukonde.

16 Mas. 69.16 Cheukirani ine ndipo ndichitireni chifundo;

pakuti ndili wounguluma ndi wozunzika.

17Masautso a mtima wanga akula,

munditulutse m'zondipsinja.

18 2Sam. 16.12 Penyani mazunzo anga ndi zovuta zanga;

ndipo khululukirani zolakwa zanga zonse.

19Penyani adani anga, popeza achuluka;

ndipo andida ndi udani wachiwawa.

20Sungani moyo wanga, ndilanditseni,

ndisakhale nao manyazi, pakuti ndakhulupirira Inu.

21Ungwiro ndi kuongoka mtima zindisunge,

pakuti ndayembekezera Inu.

22 Mas. 130.8 Ombolani Israele, Mulungu,

m'masautso ake onse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help