MIYAMBO Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mau OyambaBukuli liphunzitsa nzeru zosiyanasiyana zothandiza anthu ndi kuwongolera moyo wao wa masiku onse mwa njira yokomera Mulungu ndi anzao. Mau ake ambiri akuwoneka ngati miyambi. Mau oyamba akuti, “Kudziwa nzeru ndi mwambo; kuzindikira mau ozindikiritsa; kulandira mwambo wakusamalira machitidwe, chilungamo, chiweruzo ndi zolunjika.” Kenaka bukuli likupereka malangizo osiyanasiyana okhudza makhalidwe, kusunga mwambo, kupatsana ulemu ndi kukhalirana mwamtendere, kutsata choona ndi chilungamo, moyo wa pa banja, pa ntchito, pa malonda, pa maphwando ndi pa zochitika zina zilizonse. Nzeru ndizo zimene akuluakulu a Israele ankaphunzitsa anthu ao pa masiku akale. Wofuna kutsata nzeruzo ayenera kudzilamulira, kudzichepetsa, kuleza mtima, kulemekeza osauka ndi kukhala okhulupirika pa chibwenzi.Za mkatimuBukuli lili ndi zigawo zingapo:Mau oyamikira nzeru 1.1—9.18

Miyambi ya Solomoni 10.1—29.27

Mau a Aguri 30.1-33

Mau ena osiyanasiyana 31.1-31

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help