1 2Mbi. 34.29-32 Pamenepo mfumu inatumiza anthu, namsonkhanitsira akulu onse a Yuda ndi a mu Yerusalemu.
22Maf. 22.8Nikwera mfumu kunka kunyumba ya Yehova, ndi amuna onse a Yuda, ndi onse okhala mu Yerusalemu pamodzi naye, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi anthu onse aang'ono ndi aakulu; nawerenga iye m'makutu mwao mau onse a m'buku la chipangano adalipeza m'nyumba ya Yehova.
32Maf. 11.14, 17Niima mfumu pachiunda, ndi kuchita pangano pamaso pa Yehova, kutsata Yehova ndi kusunga malamulo ake, ndi mboni zake, ndi malemba ake, ndi mtima wonse ndi moyo wonse, kukhazikitsa mau a chipangano cholembedwa m'buku ili; ndipo anthu onse anaimiririra panganoli.
4Ndipo mfumu inalamulira Hilikiya mkulu wa ansembe, ndi ansembe a gawo lachiwiri, ndi olindira pakhomo, atulutse mu Kachisi wa Yehova zipangizo adazipangira Baala, ndi chifanizo adazipangira Baala, ndi chifanizo chija, ndi khamu lonse la kuthambo; nazitentha kunja kwa Yerusalemu ku thengo la ku Kidroni, natenga phulusa lake kunka nalo ku Betele.
5Naletsa ansembe opembedza mafano, amene mafumu a Yuda anawaika afukize zonunkhira pa misanje m'mizinda ya Yuda, ndi pamalo pozinga Yerusalemu; iwo omwe ofukizira zonunkhira Baala, ndi dzuwa, ndi mwezi, ndi nthanda, ndi khamu lonse la kuthambo.
6Natulutsa chifanizocho m'nyumba ya Yehova kunja kwa Yerusalemu ku mtsinje wa Kidroni; nachitenthera ku mtsinje wa Kidroni, nachipera chikhale fumbi, naliwaza fumbi lake pa manda a ana a anthu.
71Maf. 14.24Nagamula nyumba za anyamata adama okhala kunyumba ya Yehova, kumene akazi anaomba nsalu zolenjeka za chifanizocho.
8Natulutsa ansembe onse m'mizinda ya Yuda, nawaipitsira misanje, imene ansembe adafukizapo zonunkhira, kuyambira Geba kufikira Beereseba; napasula misanje ya kuzipata, yokhala polowera pa chipata cha Yoswa kazembe wa mzinda, yokhala ku dzanja lako lamanzere kwa chipata cha mzinda.
9Ezk. 44.10-14Koma ansembe a misanje sanakwere kudza ku guwa la nsembe la Yehova ku Yerusalemu; koma anadya mkate wopanda chotupitsa pakati pa abale ao.
10Lev. 18.21; Yes. 30.33; Yer. 7.31Anawaipitsiranso Tofeti, wokhala m'chigwa cha ana a Hinomu; kuti asapitirize mmodzi yense mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pamoto kwa Moleki.
11Nachotsanso akavalo amene mafumu a Yuda adapereka kwa dzuwa, polowera nyumba ya Yehova, ku chipinda cha Natani-Meleki mdindoyo, chokhala kukhonde; natentha magaleta a dzuwa ndi moto.
122Maf. 21.5Ndi maguwa a nsembe anali patsindwi pa chipinda chosanja cha Ahazi adawapanga mafumu a Yuda, ndi maguwa a nsembe adawapanga Manase m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova, mfumu inawagumula, niwachotsa komweko, nitaya fumbi lao ku mtsinje wa Kidroni.
131Maf. 11.7Ndipo mfumu inawaipitsira misanje yokhala kum'mawa kwa Yerusalemu, ndiyo ya ku dzanja lamanja la phiri la chionongeko, imene Solomoni mfumu ya Israele adaimangira Asitaroti chonyansa cha Asidoni, ndi Kemosi chonyansa cha Mowabu, ndi Milikomu chonyansa cha ana a Amoni.
14Eks. 23.24Nathyolathyola zoimiritsa, nalikha zifanizo, nadzaza pamalo pao ndi mafupa a anthu.
151Maf. 12.28, 33Anagumulanso guwa la nsembe linali ku Betele, ndi msanje adaumanga Yerobowamu mwana wa Nebati wolakwitsa Israele uja; guwa la nsembelo, ndi msanje womwe anagumula; natentha msanje, naupondereza ukhale fumbi, natentha chifanizo.
161Maf. 13.2Ndipo potembenuka Yosiya anaona manda okhalako kuphiri, natumiza anthu natulutsa mafupa kumanda, nawatentha paguwa la nsembe, kuliipitsa, monga mwa mau a Yehova anawalalikira munthu wa Mulungu wolalikira izi.
171Maf. 13.1, 30-31Anatinso, Chizindikiro ichi ndichiona nchiyani? Namuuza anthu a m'mzindawo, Ndicho manda a munthu wa Mulungu anafuma ku Yuda, nalalikira izi mwazichitira guwa la nsembe la ku Betele.
18Nati iye, Mlekeni, munthu asakhudze mafupa ake. Naleka iwo mafupa ake akhale pamodzi ndi mafupa a mneneri uja anatuluka mu Samariya.
192Mbi. 34.6-7Ndi nyumba zonse zomwe za ku misanje yokhala m'mizinda ya Samariya, adazimanga mafumu a Israele kuutsa nazo mkwiyo wa Yehova, Yosiya anazichotsa, nazichitira monga mwa ntchito zonse adazichita ku Betele.
20Ndipo anapha ansembe onse a misanje okhalako pa maguwa a nsembe, natentha mafupa a anthu pamenepo, nabwerera kunka ku Yerusalemu.
Achita Paska(2Mbi. 35.1-19)21 2Mbi. 35.1-19 Ndipo mfumu inalamulira anthu onse, kuti, Mchitireni Yehova Mulungu wanu Paska, monga mulembedwa m'buku ili la chipangano.
22Zedi silinachitike Paska lotere chiyambire masiku a oweruza anaweruza Israele, ngakhale m'masiku a mafumu a Israele, kapena mafumu a Yuda;
23koma Paska ili analichitira Yehova mu Yerusalemu, Yosiya atakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu.
24Lev. 19.31; 2Maf. 21.6; 22.8Ndiponso obwebweta, ndi openda, ndi aterafi, ndi mafano, ndi zonyansa zonse zidaoneka m'dziko la Yuda ndi mu Yerusalemu, Yosiya anazichotsa; kuti alimbitse mau a chilamulo olembedwa m'buku adalipeza Hilikiya wansembe m'nyumba ya Yehova.
25Ndipo asanabadwe iye panalibe mfumu wolingana naye, imene inatembenukira kwa Yehova ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse, ndi mphamvu yake yonse, monga mwa chilamulo chonse cha Mose; atafa iyeyu sanaukenso wina wolingana naye.
262Maf. 21.11-13Koma Yehova sanakhululuke mkwiyo wake waukulu waukali umene adapsa mtima nao pa Yuda, chifukwa cha zoputa zonse Manase adaputa nazo mkwiyo wake.
27Nati Yehova, Ndidzachotsa Yudanso pamaso panga, monga umo ndinachotsera Israele; ndipo ndidzataya mzinda uwu ndidausankha, ndiwo Yerusalemu, ndi nyumba ndidainena, Dzina langa lidzakhala komweko.
28Machitidwe ena tsono a Yosiya, ndi zonse anazichita, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda?
292Mbi. 35.20-24Masiku ake Farao Neko mfumu ya Aejipito anakwerera mfumu ya Asiriya ku mtsinje wa Yufurate; ndipo mfumu Yosiya anatuluka kuponyana naye, koma anapha Yosiya ku Megido, atamuona.
302Mbi. 36.1-5Ndipo anyamata ake anamtengera wakufa m'galeta, nabwera naye ku Yerusalemu kuchokera ku Megido, namuika m'manda akeake. Ndipo anthu a m'dziko anatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya, namdzoza, namlonga ufumu m'malo mwa atate wake.
Yehowahazi, Yehoyakimu ndi Yehoyakini mafumu oipa a Yuda(2Mbi. 36.2-8)31Yehowahazi anali wa zaka makumi awiri mphambu zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu miyezi itatu mu Yerusalemu ndi dzina la make ndiye Hamutala mwana wa Yeremiya wa ku Libina.
32Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga umo monse adachita makolo ake.
332Maf. 25.6Ndipo Farao Neko anammanga mu Ribula, m'dziko la Hamati; kuti asachite ufumu mu Yerusalemu; nasonkhetsa dzikoli msonkho wa matalente zana limodzi la siliva, ndi talente limodzi la golide.
34Ndipo Farao Neko analonga ufumu Eliyakimu mwana wa Yosiya, m'malo mwa Yosiya atate wake, nasanduliza dzina lake likhale Yehoyakimu; koma anapita naye Yehowahazi, nafika iye mu Ejipito, nafa komweko.
35Ndipo Yehoyakimu anapereka siliva ndi golide kwa Farao, koma anasonkhetsa dzikoli lipereke ndalamazi; monga mwa lamulo la Farao anasonkhetsa anthu a m'dziko siliva ndi golide, yense monga mwa kuyesedwa kwake, kuzipereka kwa Farao Neko.
36Yehoyakimu anali wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi chimodzi mu Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Zebida mwana wa Pedaya wa Ruma.
37Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita makolo ake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.