1Bwenzi mutandilola pang'ono ndi chopusacho! Komanso mundilole.
2Hos. 2.19-20; Agal. 4.17-18; Akol. 1.28Pakuti ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya Mulungu; pakuti ndinakupalitsani ubwenzi mwamuna mmodzi, kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwa Khristu.
3Gen. 3.4; Yoh. 8.44; Akol. 2.4, 8, 18Koma ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Khristu.
4Agal. 1.7-8Pakutitu ngati iye wakudza alalikira Yesu wina, amene ife sitinalalikire, kapena ngati mulandira mzimu wa mtundu wina, umene simunalandire, kapena Uthenga Wabwino wa mtundu wina umene simunalandire, mulolana naye bwino lomwe.
51Ako. 15.10Pakuti ndiyesa kuti sindinaperewere konse ndi atumwi oposatu.
62Ako. 12.12Ndipo ndingakhale ndili wosaphunzira m'manenedwe, koma sinditero m'chidziwitso, koma m'zonse tachionetsa kwa inu mwa anthu onse.
7Mac. 18.3; 2Ako. 12.13-14Kodi ndachimwa podzichepetsa ndekha, kuti inu mukakwezedwe, popeza ndinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu mwaufulu?
8Ndinalanda za Mipingo ina, ndi kulandira kwa iwo kulipira kuti ndikatumikire inu;
9Mac. 18.3; 20.33; 2Ako. 12.13-14ndipo pakukhala nanu, ndi kusowa, sindinasaukitse munthu aliyense; pakuti abale akuchokera ku Masedoniya, anakwaniritsa kusowa kwanga; ndipo m'zonse ndinachenjera ndekha, ndisalemetse inu, ndipo ndidzachenjerapo.
10Aro. 9.1; 1Ako. 9.15Choonadi cha Khristu chili mwa ine, kuti kudzitamandira kumene sikudzaletsedwa kwa ine mu mbali za Akaya.
11Chifukwa ninji? Chifukwa sindikonda inu kodi? Adziwa Mulungu.
121Ako. 9.12Koma chimene ndichita, ndidzachitanso, kuti ndikawadulire chifukwa iwo akufuna chifukwa; kuti m'mene adzitamandiramo, apezedwe monganso ife.
13Pakuti otere ali atumwi onyenga, ochita ochenjerera, odzionetsa ngati atumwi a Khristu.
14Ndipo kulibe kudabwa; pakuti Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika.
15Afi. 3.18-19Chifukwa chake sikuli kanthu kwakukulu ngatinso atumiki ake adzionetsa monga atumiki a chilungamo; amene chimaliziro chao chidzakhala monga ntchito zao.
Kumva zowawa kwa Paulo chifukwa cha Uthenga Wabwino16Ndinenanso, Munthu asandiyese wopanda nzeru; koma ngati mutero, mundilandirenso ine monga wopanda nzeru, kuti inenso ndidzitamandire pang'ono.
17Chimene ndilankhula sindilankhula monga mwa Ambuye, koma monga wopanda nzeru, m'kulimbika kumene kwa kudzitamandira.
18Afi. 3.3-4Popeza ambiri adzitamandira monga mwa thupi, inenso ndidzadzitamandira.
19Pakuti mulolana nao opanda nzeru mokondwera, pokhala anzeru inu nokha.
20Agal. 2.4Pakuti mulola ngati wina akuyesani inu akapolo, ngati wina alikwira inu, ngati wina alanda zanu, ngati wina adzikuza, ngati wina akupandani pankhope.
21Afi. 3.3-4Ndinena monga mwa kunyoza, monga ngati tinakhala ofooka. Koma m'mene wina alimbika mtimamo (ndinena mopanda nzeru) momwemo ndilimbika mtima inenso.
22Mac. 22.13Kodi ali Ahebri? Inenso. Kodi ali Aisraele? Inenso. Kodi ali mbeu ya Abrahamu? Inenso.
23Deut. 25.3; 1Ako. 15.10; 2Ako. 6.4-5Kodi ali atumiki a Khristu? (Ndilankhula monga moyaluka), makamaka ine; m'zivutinso mochulukira, m'ndende mochulukira, m'mikwingwirima mosawerengeka, muimfa kawirikawiri.
24Kwa Ayuda ndinalandira kasanu mikwingwirima makumi anai kuperewera umodzi.
25Mac. 14.19; 16.22; 27.41Katatu ndinamenyedwa ndi ndodo, kamodzi ndinaponyedwa miyala, katatu ndinatayika posweka chombo, ndinakhala m'kuya tsiku limodzi usana ndi usiku;
26Mac. 9.23; 13.50paulendo kawirikawiri, moopsa mwake mwa mitsinje, moopsa mwake mwa olanda, moopsa modzera kwa mtundu wanga, moopsa modzera kwa amitundu, moopsa m'mzinda, moopsa m'chipululu, moopsa m'nyanja, moopsa mwa abale onyenga;
271Ako. 4.11m'chivutitso ndi m'cholemetsa, m'madikiro kawirikawiri, m'njala ndi ludzu, m'masalo a chakudya kawirikawiri, m'chisanu ndi umaliseche.
28Popanda zakunjazo pali chondisindikiza tsiku ndi tsiku, chalabadiro cha Mipingo yonse.
291Ako. 9.22Afooka ndani wosafooka inenso? Akhumudwitsidwa ndani, wosatenthanso ine?
302Ako. 12.5Ngati ndiyenera kudzitamandira, ndidzadzitamandira ndi za kufooka kwanga.
31Mulungu Atate wa Ambuye Yesu, Iye amene alemekezeka kunthawi yonse, adziwa kuti sindinama.
32Mac. 9.24-25Mu Damasiko kazembe wa mfumu Areta analindizitsa mzinda wa Adamasiko kuti andigwire ine;
33ndipo mwa zenera, mudengu, ananditsitsa pakhoma, ndipo ndinapulumuka m'manja mwake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.