1Ndipo Yobu anaonjezanso mwambi wake, nati,
2Pali Mulungu, amene anandichotsera zoyenera ine,
ndi Wamphamvuyonse, amene anawawitsa moyo wanga,
3pakuti moyo wanga wonse ukali mwa ine,
ndi mpweya wa Mulungu m'mphuno mwanga;
4milomo yanga siilankhula chosalungama,
ndi lilime langa silitchula zachinyengo.
5Sindivomereza konse kuti muli olungama;
mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga.
6 Mac. 24.16 Ndiumirira chilungamo changa, osachileka;
chikhalire moyo ine, mtima wanga sunditonza.
7Mdani wanga akhale ngati woipa,
ndi iye amene andiukira ngati wosalungama.
8 Mat. 16.26 Pakuti chiyembekezo cha wonyoza Mulungu nchiyani pomlikhatu Mulungu,
pomchotsera moyo wake?
9 Mas. 18.41; Yes. 1.15; Yoh. 9.31; Yak. 4.3 Kodi Mulungu adzamvera kufuula kwake, ikamdzera nsautso?
10Kodi adzadzikondweretsa naye Wamphamvuyonse,
ndi kuitana kwa Mulungu nthawi zonse?
11Ndidzakulangizani za dzanja la Mulungu;
chokhala ndi Wamphamvuyonse sindidzachibisa.
12Taonani, inu nonse munachiona;
ndipo mugwidwa nazo zopanda pake chifukwa ninji?
13Ili ndi gawo la munthu woipa kwa Mulungu,
ndi cholowa cha akupsinja anzao achilandira kwa Wamphamvuyonse.
14 Deut. 28.41 Akachuluka ana ake, ndiko kuchulukira lupanga,
ndi ana ake sadzakhuta chakudya.
15Akumtsalira iye adzaikidwa muimfa,
ndi akazi ake amasiye sadzalira maliro.
16Chinkana akundika ndalama ngati fumbi,
ndi kukonzeratu zovala ngati dothi;
17 Miy. 28.8; 13.22 azikonzeretu, koma wolungama adzazivala,
ndi wosalakwa adzagawa ndalamazo.
18Amanga nyumba yake ngati kangaude,
ndi ngati wolindira amanga dindiro.
19Agona pansi ali wachuma, koma saikidwa;
potsegula maso ake, wafa chikomo.
20Zoopsa zimgwera ngati madzi;
nkuntho umtenga usiku.
21Mphepo ya kum'mawa imtenga, nachoka iye;
nimkankha achoke m'malo mwake.
22Pakuti Mulungu adzamponyera zoopsa, osamleka;
kuthawa akadathawa m'dzanja lake.
23Anthu adzamuombera manja,
nadzamuimbira mluzu achoke m'malo mwake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.