1 Mas. 70.5 Yehova, ndaitana kwa Inu; ndifulumireni ine;
munditcherere khutu, pamene ndiitana kwa Inu.
2 Chiv. 8.3-4 Pemphero langa liikike ngati chofukiza pamaso panu;
kukweza manja anga kuikike ngati nsembe ya madzulo.
3Muike mdindo pakamwa panga, Yehova;
sungani pakhomo pa milomo yanga.
4 Miy. 23.6 Mtima wanga usalinge kuchinthu choipa,
kuchita ntchito zoipa
ndi anthu akuchita zopanda pake;
ndipo ndisadye zankhuli zao.
5 Miy. 9.8; 19.25; 25.12 Akandipanda munthu wolungama ndidzati nchifundo:
akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu;
mutu wanga usakane:
Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera.
6Oweruza ao anagwetseka pambali pa thanthwe;
nadzamva mau anga kuti ndiwo okondweretsa.
7Mafupa athu amwazika pakamwa pa manda,
monga ngati akumba nanyimphula nthaka yapansi.
8 2Mbi. 20.12 Pakuti maso anga apenya kwanu, Yehova Ambuye;
ndithawira kwa Inu; musataye moyo wanga.
9 Mas. 119.110 Mundisunge ndisagwe mumsampha ananditcherawo,
ndisakodwe m'makwekwe a iwo ochita zopanda pake.
10 Mas. 35.8 Oipa agwe pamodzi m'maukonde ao,
kufikira nditapitirira ine.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.