1Ndilanditseni, Yehova, kwa munthu woipa;
ndisungeni kwa munthu wachiwawa;
2amene adzipanga zoipa mumtima mwao;
masiku onse amemeza nkhondo.
3 Aro. 3.13 Anola lilime lao ngati njoka;
pansi pa milomo yao pali ululu wa mphiri.
4 Mas. 71.4 Ndilindireni Yehova, ndisalowe m'manja mwa woipa;
ndisungeni kwa munthu wachiwawa;
kwa iwo akuti akankhe mapazi anga.
5 Yer. 18.22 Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe;
anatcha ukonde m'mphepete mwa njira;
ananditchera makwekwe.
6Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga;
munditcherere khutu mau a kupemba kwanga, Yehova.
7Yehova Ambuye, ndinu mphamvu ya chipulumutso changa,
munandiphimba mutu wanga tsiku lakulimbana nkhondo.
8Yehova, musampatse woipa zokhumba iye;
musamthandize zodzipanga zake; angadzikuze.
9 Miy. 18.7 Kunena za mutu wao wa iwo akundizinga,
choipa cha milomo yao chiwaphimbe.
10Makala amoto awagwere;
aponyedwe kumoto;
m'maenje ozama, kuti asaukenso.
11Munthu wamlomo sadzakhazikika padziko lapansi;
choipa chidzamsaka munthu wachiwawa kuti chimgwetse.
12 1Maf. 8.45 Ndidziwa kuti Yehova adzanenera wozunzika mlandu,
ndi kuweruzira aumphawi.
13 Mas. 11.7 Indedi, olungama adzayamika dzina lanu;
oongoka mtima adzakhala pamaso panu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.