1 2Sam. 15.18 Yehova! Ha! Achuluka nanga akundisautsa ine!
Akundiukira ine ndi ambiri.
2 Mas. 71.11 Ambiri amati kwa moyo wanga,
alibe chipulumutso mwa Mulungu.
3 Gen. 15.1; Mas. 28.7 Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa;
ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga.
4 Mas. 34.4 Ndifuula kwa Yehova ndi mau anga,
ndipo andiyankha m'phiri lake loyera.
5 Mas. 4.8 Ndinagona ine pansi, ndinagona tulo;
ndinauka; pakuti Yehova anandichirikiza.
6 Mas. 27.3 Sindidzaopa unyinji wa anthu akundizinga ine.
7 Mas. 7.6 Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga!
Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya;
mwawathyola mano oipawo.
8 Yes. 43.11 Chipulumutso ncha Yehova;
dalitso lanu likhale pa anthu anu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.