1Ndipo Yobu anaonjezanso mwambi wake, nati,
2Ha! Ndikadakhala monga m'miyezi yapitayi,
monga m'masiku akundisunga Mulungu;
3 Mas. 18.28 muja nyali yake inawala pamutu panga,
ndipo ndi kuunika kwake ndinayenda mumdima;
4monga umo ndinakhala m'masiku anga olimba,
muja uphungu wa Mulungu unakhala pahema panga.
5Muja Wamphamvuyonse akali nane pamodzi,
ndi ana anga anandizinga;
6 Deut. 32.13-14 muja popondera ine padakhatamira ndi mafuta amkaka,
ndi thanthwe linanditsanulira mitsinje ya mafuta a azitona!
7Muja ndinatuluka kunka kuchipata kumzinda,
muja ndinakonza pokhala panga kukhwalala,
8anyamata anandiona nabisala,
okalamba anandinyamukira, nakhala chilili.
9Akalonga anadziletsa kulankhula,
ndi kugwira pakamwa pao;
10 Mas. 137.6 mau a omveka anali zii,
ndi lilime lao linamamatira kumalakalaka ao.
11Pakuti pondimva ine khutu, linandidalitsa;
ndipo pondiona diso, linandichitira umboni.
12 Miy. 21.13; Yob. 22.9 Pakuti ndinapulumutsa wozunzika wakufuula;
mwana wamasiye yemwe wosowa mthandizi.
13Dalitso la iye akati atayike linandidzera,
ndi mtima wa mkazi wamasiye ndinauimbitsa mokondwera.
14 Yes. 61.10; Aef. 6.1 Ndinavala chilungamo, ndipo chinandivala ine;
chiweruzo changa chinanga mwinjiro ndi nduwira.
15 Num. 10.31 Ndinali maso a akhungu,
ndi mapazi a otsimphina.
16 Miy. 29.7 Ndinali atate wa waumphawi;
ndi mlandu wa iye amene sindinamdziwe ndinafunsitsa.
17Ndipo ndinathyola nsagwada ya wosalungama,
ndi kukwatula chogwidwa kumano kwake.
18Pamenepo ndinati, Ndidzatsirizika m'chisa changa;
ndipo ndidzachulukitsa masiku anga ngati mchenga.
19 Mas. 1.3; Yer. 17.8 Muzu wanga watambalala kufikira kumadzi;
ndi mame adzakhala pa nthambi yanga usiku wonse.
20Ulemu wanga udzakhala wosaguga mwa ine,
ndi uta wanga udzakhala wosalifuka m'dzanja mwanga.
21Anthu anandimvera, nalindira,
nakhala chete, kuti ndiwapangire.
22Nditanena mau anga sanalankhulenso,
ndi kunena kwanga kunawakhera.
23Anandilindira ngati kulindira mvula,
nayasama pakamwa pao ngati kulira mvula ya masika.
24Ndinawaseka akapanda kulimbika mtima;
ndipo sanagwetse kusangalala kwa nkhope yanga.
25Ndinawasankhira njira yao ndi kukhala mkulu wao.
Ndinakhala ngati mfumu mwa ankhondo ake,
ngati wotonthoza ofedwa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.