OBADIYA Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu
Mau OyambaMneneriyu adalalikira mau ake pa nthawi ina yosadziwika bwinobwino Yerusalemu atangopasuka kumene m'chaka cha 586 BC. Nthawi imeneyo, Edomu anasangalala atamva kuti Yerusalemu wagwa. Edomu anali mdani wa Ayuda kuyambira kalekale wa dera lakum'mwera chakumadzulo. Sipokhapo ai, iye anatengerapo mwai pa chipsinjo cha Yuda pofunkha katundu wolandidwa ndi kumuthandizira mdaniyo. Obadiya analosera kuti Edomu adzalangidwa ndi kugonjetsedwa, pamodzi ndi maiko ena onse amene anali adani a Israele.Za mkatimuChilango cha Edomu 1-14 Tsiku la Ambuye 15-21