1Anandisautsa kawirikawiri kuyambira ubwana wanga,
anene tsono Israele;
2 Yoh. 16.33 Anandisautsa kawirikawiri kuyambira ubwana wanga;
koma sanandilake.
3Olima analima pamsana panga;
anatalikitsa mipere yao.
4Yehova ndiye wolungama;
anadulatu zingwe za oipa.
5Achite manyazi nabwerere m'mbuyo.
Onse akudana naye Ziyoni.
6 Mas. 37.2 Akhale ngati udzu womera patsindwi,
wakufota asanauzule;
7umene womweta sadzaza nao dzanja lake,
kapena womanga mitolo sakupatira manja.
8 Rut. 2.4; Mas. 118.26; Yes. 8.18 Angakhale opitirirapo sanena,
Dalitso la Mulungu likhale pa inu;
tikudalitsani m'dzina la Yehova.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.