YOBU 4 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Elifazi adzudzula Yobu(4.1—14.22)

1Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati,

2Munthu akayesa kunena nawe mau,

kodi udzamva nao chisoni?

Koma akhoza ndani kudziletsa kunena?

3 Yes. 35.3 Taona iwe walangiza aunyinji,

walimbitsa manja a ofooka.

4 Yes. 35.3 Mau ako anachirikiza iye amene akadagwa,

walimbitsanso maondo otewa.

5Koma tsopano chakufikira iwe, ndipo ukomoka;

chikukhudza, ndipo uvutika.

6 Miy. 3.26 Kodi kulimbika mtima kwako si ndiko kuti uopa Mulungu,

ndi chiyembekezo chako si ndiwo ungwiro wa njira zako?

7 Mas. 37.25 Takumbukira tsopano, watayika ndani wosapalamula konse?

Kapena oongoka mtima alikhidwa kuti?

8 Miy. 22.8; Agal. 6.7 Monga umo, ndaonera, olimira mphulupulu,

nabzala vuto, akololapo zomwezo.

9Atayika ndi mpweya wa Mulungu,

nathedwa ndi mpumo wa mkwiyo wake.

10Kubangula kwa mkango,

ndi kulira kwa mkango waukali kwaletsedwa,

ndi mano a misona ya mkango athyoledwa.

11Mkango wokalamba udzifera posowa mkoka,

ndi misona ya mkango waukazi imwazika.

12Anditengera mau m'tseri,

m'khutu mwanga ndinalandira kunong'oneza kwake.

13M'malingaliro a masomphenya a usiku,

powagwira anthu tulo tatikulu

14Anandidzera mantha ndi kunjenjemera,

nanthunthumira nako mafupa anga onse.

15Pamenepo panapita mzimu pamaso panga;

tsitsi la thupi langa lidati nyaunyau.

16Unaima chilili, koma sindinathe kuzindikira maonekedwe ake;

panali mzukwa pamaso panga;

kunali chete, ndipo ndidamva mau akuti,

17 Yob. 9.2 Kodi munthu adzakhala wolungama ndi kuposa Mulungu?

Kodi munthu adzakhala woyera woposa Mlengi wake?

18Taona, sakhulupirira atumiki ake;

nawanenera amithenga ake zopusa;

19 2Ako. 4.7; 5.1 kopambana kotani nanga iwo akukhala m'nyumba zadothi,

amene kuzika kwao kuli m'fumbi,

angothudzulidwa ngati njenjete.

20 Mas. 90.5-6 Kuyambira m'mawa kufikira madzulo athudzuka;

aonongeka kosatha, osasamalirako munthu.

21Kukometsetsa kwao sikumachotsedwa nao?

Amafa koma opanda nzeru.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help