MLALIKI 12 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 Miy. 22.6 Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako, asanadze masiku oipa, ngakhale zisanayandikire zakazo zakuti udzati, Sindikondwera nazo;

2ngakhale lisanade dzuwa, ndi kuunika, ndi mwezi, ndi nyenyezi, mitambo ndi kubweranso italeka mvula;

3tsikulo omwe asunga nyumba adzanthunthumira, amuna olimba nadzawerama, akupera nadzaleka poperewera, omwe ayang'ana pamazenera nadzadetsedwa;

4pa khomo lakunja padzatsekeka; potsika mau akupera, wina nanyamuka polira mbalame, ndipo akazi onse akuimba sadzamveka bwino;

5Yob. 17.13-16; Yer. 9.17-18inde, adzaopa za pamwamba, panjira padzakhala zoopsa; katungurume adzaphuka, dzombe ndi kukoka miyendo, zilakolako ndi kutha; pakuti munthu apita kwao kwamuyaya, akulira maliro nayendayenda panja;

6chingwe chasiliva chisanaduke, ngakhale mbale yagolide isanasweke, ngakhale mtsuko usanaphwanyike kukasupe, ngakhale njinga yotungira madzi isanathyoke kuchitsime;

7Gen. 3.19; Num. 16.22; Zek. 12.1fumbi ndi kubwera pansi pomwe linali kale, mzimu ndi kubwera kwa Mulungu amene anaupereka.

8Mlal. 1.2Chabe zachabetu, ati Mlalikiyo; zonse ndi chabe.

Zoyenera munthu ndizo kuopa Mulungu ndi kusunga malamulo ake

9Ndiponso pokhala wanzeru Mlalikiyo anaphunzitsabe anthu nzeru; inde, anatchera makutu nafunafuna nalongosola miyambi yambiri.

10Mlalikiyo anasanthula akapeze mau okondweretsa, ndi zolemba zoongoka ngakhale mau oona.

11Mau a anzeru akunga zisonga, omwe akundika mau amene mbusa mmodzi awapatsa mau ao akunga misomali yokhomedwa zolimba.

12Pamodzi ndi izi, mwananga, tachenjezedwa; pakuti saleka kulemba mabuku ambiri; ndipo kuphunzira kwambiri kutopetsa thupi.

13 Deut. 10.12 Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.

14Mat. 12.36; Mac. 17.30-31; Aro. 2.16; 2Ako. 5.10Pakuti Mulungu adzanena mlandu wa zochita zonse, ndi zobisika zonse, ngakhale zabwino ngakhale zoipa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help