1 Yow. 2.31 Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa. Adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.
2Luk. 1.78; Aef. 5.14Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m'mapiko mwake; ndipo mudzatuluka ndi kutumphatumpha ngati anaang'ombe onenepa otuluka m'khola.
3Ndipo mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala ngati mapulusa kumapazi anu, tsiku ndidzaikalo, ati Yehova wa makamu.
4 Eks. 20.3-17; Deut. 4.10 Kumbukirani chilamulo cha Mose mtumiki wanga, ndinamlamuliracho mu Horebu chikhale cha Israele yense, ndicho malemba ndi maweruzo.
5Yow. 2.31; Mat. 11.13-14; 17.11Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.
6Zek. 14.12Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate ao; kuti ndisafike ndi kukantha dziko lionongeke konse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.