1 Mas. 121.3-5 Akapanda kumanga nyumba Yehova,
akuimanga agwiritsa ntchito chabe;
akapanda kusunga mzinda Yehova,
mlonda adikira chabe.
2 Gen. 3.17, 19 Kuli chabe kwa inu kulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo,
kudya mkate wosautsa kuupeza;
kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ake ngati m'tulo.
3 Gen. 33.5; Yos. 24.3 Taonani, ana ndiwo cholowa cha kwa Yehova;
chipatso cha m'mimba ndicho mphotho yake.
4Ana a ubwana wake wa munthu
akunga mivi m'dzanja lake la chiphona.
5 Miy. 27.11 Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake:
sadzachita manyazi iwo,
pakulankhula nao adani kuchipata.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.