AHEBRI 4 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 Aheb. 12.15 Chifukwa chake tiope kuti kapena likatsala lonjezano lakulowa mpumulo wake, wina wa inu angaoneke ngati adaliperewera.

2Pakuti kwa ifenso walalikidwa Uthenga Wabwino, monganso kwa iwo; koma iwowa sanapindule nao mau omvekawo, popeza sanasakanizike ndi chikhulupiriro mwa iwo amene adawamva.

3Mas. 95.11Popeza ife amene takhulupirira tilowa mpumulowo, monga momwe ananena,

Monga ndalumbira mu mkwiyo wanga,

ngati adzalowa mpumulo wanga.

Zingakhale ntchitozo zidatsirizika kuyambira kuzika kwa dziko lapansi.

4Gen. 2.2; Eks. 20.11Pakuti wanena pena za tsiku lachisanu ndi chiwiri, natero, Ndipo Mulungu anapumula tsiku lachisanu ndi chiwiri, kuleka ntchito zake zonse.

5Ndipo m'menemonso,

Ngati adzalowa mpumulo wanga.

6 Aheb. 3.19 Popeza tsono patsala kuti ena akalowa momwemo, ndi iwo amene Uthenga Wabwino unalalikidwa kwa iwo kale sanalowemo chifukwa cha kusamvera,

7Mas. 95.7alangizanso tsiku lina, ndi kunena mu Davide, itapita nthawi yaikulu yakuti, Lero, monga kwanenedwa kale,

Lero ngati mudzamva mau ake,

musaumitse mitima yanu.

8Pakuti ngati Yoswa akadawapumitsa iwo, sakadalankhula m'tsogolomo za tsiku lina.

9Momwemo utsalira mpumulo wa Sabata wa kwa anthu a Mulungu.

10Pakuti iye amene adalowa mpumulo wake, adapumulanso mwini wake kuntchito zake, monganso Mulungu kuzake za Iye.

11Aheb. 3.12, 18-19Chifukwa chake tichite changu cha kulowa mpumulowo, kuti wina angagwe m'chitsanzo chomwe cha kusamvera.

12Yes. 49.2; Aef. 6.17; 1Ako. 14.24-25Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.

13Mas. 139.11-12; Miy. 15.11Ndipo palibe cholembedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.

Khristu aposa akulu a ansembe

14 Aheb. 3.1; 7.26 Popeza tsono tili naye Mkulu wa ansembe wamkulu, wopyoza miyamba, Yesu mwana wa Mulungu, tigwiritsitse chivomerezo chathu.

15Yes. 53.3; Aheb. 2.18; Luk. 22.28; 2Ako. 5.21; Aheb. 7.26Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.

16Aef. 2.18; 3.12Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help