2 AKORINTO 6 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Kudzikana kwa Paulo mu utumiki wake

1 Yes. 49.8; 1Ako. 3.9 Ndipo ochita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu,

2(pakuti anena,

M'nyengo yolandiridwa ndinamva iwe,

ndipo m'tsiku la chipulumutso ndinakuthandiza.

Taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la chipulumutso);

3Aro. 14.13osapatsa chokhumudwitsa konse m'chinthu chilichonse, kuti utumikiwo usanenezedwe;

41Ako. 4.1koma m'zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu, m'kupirira kwambiri, m'zisautso, m'zikakamizo, m'zopsinja,

52Ako. 11.23-27m'mikwingwirima, m'ndende, m'maphokoso, m'mavutitso, m'madikiro, m'masalo a chakudya;

6m'mayeredwe, m'chidziwitso, m'chilekerero, m'kukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, m'chikondi chosanyenga;

7m'mau a choonadi, mu mphamvu ya Mulungu; mwa zida za chilungamo kulamanja ndi kulamanzere,

8mwa ulemerero, mwa mnyozo, mwa mbiri yoipa ndi mbiri yabwino; monga osocheretsa, angakhale ali oona;

91Ako. 4.9-12monga osadziwika, angakhale adziwika bwino; monga alinkufa, ndipo taonani tili ndi moyo; monga olangika, ndipo osaphedwa;

10monga akumva chisoni, koma akukondwera nthawi zonse; monga aumphawi, koma akulemeretsa ambiri; monga okhala opanda kanthu, ndipo akhala nazo zinthu zonse.

Awadandaulira akhale oyera mtima

11M'kamwa mwathu mmotseguka kwa inu Akorinto, mtima wathu wakulitsidwa.

12Simupsinjika mwa ife, koma mupsinjika mumtima mwanu.

13Ndipo kukhale chibwezero chomwechi (ndinena monga ndi ana anga) mukulitsidwe inunso.

141Maf. 18.21; 1Ako. 5.9; Aef. 5.7, 11Musakhale omangidwa m'goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima?

15Ndipo Khristu avomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupirira?

16Lev. 26.12; 1Ako. 3.16; 6.19Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi Kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife Kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.

172Ako. 7.1; Chiv. 18.4Chifukwa chake,

Tulukani pakati pao, ndipo patukani, ati Ambuye,

Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka;

ndipo Ine ndidzalandira inu,

18 Yer. 31.9 ndipo ndidzakhala kwa inu Atate,

ndi inu mudzakhala kwa Ine ana aamuna ndi aakazi,

anena Ambuye Wamphamvuyonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help