NUMERI 22 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Za Balamu ndi Balaki

1Ndipo ana a Israele anayenda ulendo, namanga mahema m'zigwa za Mowabu, tsidya la Yordani ku Yeriko.

2Ndipo Balaki mwana wa Zipori anaona zonse Israele anachitira Aamori.

3Eks. 15.15Ndipo Mowabu anachita mantha akulu ndi anthuwo, popeza anachuluka; nada mtima Mowabu chifukwa cha ana a Israele.

4Ndipo Mowabu anati kwa akulu a Midiyani, Tsopano msonkhano uwu udzanyambita zonse zili pozinga pathu, monga ng'ombe zinyambita msipu wa kubusa. Ndipo Balaki mwana wa Zipori anali mfumu ya Mowabu masiku amenewo.

5Mik. 6.5; 2Pet. 2.15; Yud. 1.11; Chiv. 2.14Ndipo anatuma amithenga kwa Balamu mwana wa Beori, ku Petori, wokhala kumtsinje, wa dziko la anthu a mtundu wake, kuti amuitane, ndi kuti, Taonani, anatuluka anthu m'dziko la Ejipito; taonani, aphimba nkhope ya dziko, nakhala popenyana ndi ine.

6Ndipo tsopano, idzatu, nunditembererere anthu awa; popeza andiposa mphamvu; kapena ndidzawapambana, kuti tiwakanthe, ndi kuti ndiwapirikitse m'dziko; pakuti ndidziwa kuti iye amene umdalitsa adalitsika, ndi iye amene umtemberera atemberereka.

71Sam. 9.7-8Ndipo akulu a Mowabu ndi akulu a Midiyani anamuka ndi mphotho za maula m'dzanja lao; anadza kwa Balamu, nanena naye mau a Balaki.

8Ndipo ananena nao, Mugone kuno usiku uno, ndidzakubwezerani mau, monga Yehova adzanena ndi ine; pamenepo mafumu a Mowabu anagona ndi Balamu.

9Gen. 20.3Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu, nati, Anthu awa ali ndi iwe ndiwo ayani?

10Ndipo Balamu anati kwa Mulungu, Balaki mwana wa Zipori mfumu ya Mowabu, anatumiza kwa ine, ndi kuti,

11Taonani, anthu awa adatuluka mu Ejipito aphimba nkhope ya dziko, idzatu unditembererere awa; kapena ndidzakhoza kulimbana nao nkhondo, ndi kuwapirikitsa.

12Koma Mulungu anati kwa Balamu, Usapita nao; usatemberera anthuwa; pakuti adalitsika.

13Ndipo Balamu anauka m'mawa, nati kwa akalonga a Balaki, Mukani ku dziko lanu; popeza Yehova andikaniza kuti ndisapite nanu.

14Pamenepo akalonga a Mowabu ananyamuka, nafika kwa Balaki, nati Alikukana Balamu kudza nafe.

15Koma Balaki anaonjeza kutumanso akalonga, ochuluka, ndi omveka koposa awa.

16Ndipo anadza kwa Balamu, nati kwa iye, Atero Balaki mwana wa Zipori, Pasakhaletu chinthu chakukuletsa kudza kwa ine;

17popeza ndidzakuchitira ulemu waukulu, ndipo zonse unena ndi ine ndidzachita; chifukwa chake idzatu, unditembererere anthu awa.

18Num. 24.13; 1Maf. 22.14Ndipo Balamu anayankha nati kwa anyamata a Balaki, Chinkana Balaki andipatsa nyumba yake yodzala ndi siliva ndi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova Mulungu wanga, kuchepsako kapena kuonjezako.

19Ndikupemphani, tsono, khalani pano inu usiku uno womwe; kuti ndidziwe chomwe Yehova adzanenanso nane.

20Num. 22.9; 23.12Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu usiku, nanena naye, Akadza kukuitana anthuwa, nyamuka, kunka nao, koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukachite.

21Pamenepo Balamu anauka m'mawa namanga bulu wake, namuka nao akalonga a ku Mowabu.

221Mbi. 21.16Koma anapsa mtima Mulungu chifukwa cha kupita iye, ndipo mthenga wa Yehova anadziika m'njira wotsutsana naye. Ndipo anali wokwera pabulu wake, ndi anyamata ake awiri anali naye.

23Ndipo buluyo anaona mthenga wa Yehova alikuima m'njira, ndi lupanga lake ku dzanja lake; ndi bulu anapatuka m'njira, nalowa kuthengo; ndipo Balamu anampanda bulu kumbwezera kunjira.

24Pamenepo mthenga wa Yehova anaima m'njira yopapatiza ya minda yampesa; mbali ina kuli linga, mbali ina linga.

25Ndipo bulu anaona mthenga wa Yehova, nadzikankhira kulinga, nakanikiza phazi la Balamu kulinga; ndipo anampandanso.

26Pamenepo mthenga wa Yehova anapitiriranso, naima popapatiza, popanda popatukira kulamanja kapena kulamanzere.

27Ndipo bulu wake anaona mthenga wa Yehova, nagona pansi, Balamu ali pamsana pake; ndipo Balamu adapsa mtima, nampanda bulu ndi ndodo.

282Pet. 2.16Ndipo Yehova anatsegula pakamwa pake pa bulu, nati uyu kwa Balamu, Ndakuchitanji, kuti wandipanda katatu tsopano?

29Pamenepo Balamu anati kwa bulu, Chifukwa wandipeputsa; mukadakhala lupanga m'dzanja langa tsopano, ndikadakupha iwe.

30Ndipo bulu anati kwa Balamu, Si ndine bulu wako amene umayenda wokwera pa ine chiyambire ndili wako kufikira lero lino? Kodi ndikakuchitira chotere ndi kale lonse? Ndipo anati, Iai.

312Maf. 6.17; Luk. 24.31Pamenepo Yehova anapenyetsa maso a Balamu, naona iye mthenga wa Yehova alikuima m'njira, lupanga losolola lili kudzanja, ndipo anawerama mutu wake, nagwa nkhope yake pansi.

32Ndipo mthenga wa Yehova ananena naye, Wapandiranji bulu wako katatu tsopano? Taona, ndatuluka kuti nditsutsane nawe popeza njira iyi ikugwetsa chamutu pamaso panga;

33koma bulu anandiona, nandipatukira nthawi izi zitatu pondiona; akadapanda kundipatukira, ndikadakupha iwe ndithu, ndi kumsunga iye wamoyo.

341Sam. 15.24; 2Sam. 12.13Pamenepo Balamu anati kwa mthenga wa Yehova, Ndachimwa, popeza sindinadziwe kuti munaima mondiletsa m'njira; ndipo tsopano, ngati chikuipirani, ndibwerera.

35Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa Balamu, Pita nao anthuwa; koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukanene. Potero Balamu anamuka nao akalonga a Balaki.

36Pamene Balaki anamva kuti wafika Balamu, anamtulukira kukakomana naye kumzinda wa Mowabu, wokhala m'mphepete mwa Arinoni, ndiwo ku malekezero a malire ake.

37Num. 22.17; 24.11Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Kodi sindinatumize kwa iwe ndithu kukakuitana? Unalekeranji kudza kwa ine? Sindikhoza kodi kukuchitira ulemu?

38Num. 23.26; 1Maf. 22.14Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Taonani, ndafika kwa inu; ngati ndili nayo mphamvu konse tsopano kunena kanthu? Mau amene Mulungu aike m'kamwa mwanga ndiwo ndidzanena.

39Ndipo Balamu anamuka ndi Balaki, nafika iwo ku Kiriyati-Huzoti.

40Pamenepo Balaki anapha ng'ombe ndi nkhosa, natumizira Balamu, ndi akalonga okhala naye.

41Ndipo kunali kuti m'mawa, Balaki anatenga Balamu, nakwera naye ku misanje ya Baala, ndi kumeneko anaona malekezero a anthuwo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help