1 Yes. 48.11 Kwa ife ai, Yehova, kwa ife ai,
koma kwa dzina lanu patsani ulemerero,
chifukwa cha chifundo chanu, ndi choonadi chanu.
2 Mas. 42.3; Yow. 2.17 Aneneranji amitundu,
Ali kuti Mulungu wao?
3 1Mbi. 16.26 Koma Mulungu wathu ndiye ali m'mwamba;
achita chilichonse chimkonda.
4 Mas. 135.15-18 Mafano ao ndiwo a siliva ndi golide,
ntchito za manja a anthu.
5Pakamwa ali napo, koma osalankhula;
maso ali nao, koma osapenya;
6makutu ali nao, koma osamva;
mphuno ali nazo, koma osanunkhiza;
7manja ali nao, koma osagwira;
mapazi ali nao, koma osayenda;
kapena sanena pammero pao.
8 Hab. 2.18-19 Adzafanana nao iwo akuwapanga;
ndi onse akuwakhulupirira.
9 Mas. 62.8 Israele, khulupirira Yehova:
Ndiye mthandizi wao ndi chikopa chao.
10 Mas. 118.3 Nyumba ya Aroni, khulupirira Yehova:
Ndiye mthandizi wao, ndi chikopa chao.
11Inu akuopa Yehova, khulupirirani Yehova;
ndiye mthandizi wao ndi chikopa chao.
12Yehova watikumbukira; adzatidalitsa:
adzadalitsa nyumba ya Israele;
adzadalitsa nyumba ya Aroni.
13 Mas. 128.1-4 Adzadalitsa iwo akuopa Yehova,
aang'ono ndi aakulu.
14Yehova akuonjezereni dalitso,
inu ndi ana anu.
15Odalitsika inu a kwa Yehova,
wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.
16Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova;
koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.
17 Yes. 38.18 Akufa salemekeza Yehova,
kapena aliyense wakutsikira kuli chete:
18 Dan. 2.20 Koma ife tidzalemekeza Yehova
kuyambira tsopano kufikira nthawi yonse.
Aleluya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.