1 Mlal. 1.12 Mau a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya mu Yerusalemu.
2Mas. 39.5-6; Mlal. 12.8; Aro. 8.20Zachabechabe, ati Mlaliki; zachabechabe zonse ndi chabe.
3Kodi ntchito zake zonse munthu asauka nazo zimpindulira chiyani?
4Mas. 90.5Mbadwo wina upita, mbadwo wina nufika; koma dziko lingokhalabe masiku onse.
5Mas. 19.5-6Inde dzuwa lituluka, nililowa, nilifulumira komwe linatulukako.
6Yoh. 3.8Kulowa kumwera ndi kuzungulira kumpoto zungulirezungulire imaomba mphepo; ibweranso monga mwa mazunguliridwe ake.
7Mitsinje yonse ithira m'nyanja, koma nyanja yosadzala; komwe imukira mitsinjeyo, komweko ibweranso.
8Miy. 27.20Zinthu zonse zilemetsa; munthu sangathe kuzifotokoza; maso sakhuta m'kuona, ndi makutu sakhuta m'kumva.
9Chomwe chinaoneka chidzaonekanso; ndi chomwe chinachitidwa chidzachitidwanso; ndipo palibe kanthu katsopano pansi pano.
10Kodi pali kanthu unganene kuti, Taona katsopano aka? Kanalipo kale, kale lomwe tisanabadwe ife.
11Zoyamba zija sizikumbukiridwa; ngakhale zomwe zilinkudzazo, omwe adzakhalabe m'tsogolomo, sadzazikumbukirai.
12Ine Mlaliki ndinali mfumu ya Israele mu Yerusalemu.
13Gen. 3.19Ndipo ndinapereka mtima kufunafuna ndi nzeru, ndi kulondetsa zonse zimachitidwa pansi pa thambo; ntchito yovuta imeneyi Mulungu apatsa ana a anthu akasauke nayo.
14Ndaona ntchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
15Chokhotakhota sichingaongokenso; ndipo choperewera sichingawerengedwe.
161Maf. 3.12-13Ndinalankhula ndi mtima wanga, ndi kuti, Taona, ndakuza ndi kudzienjezera nzeru koposa onse anakhala mu Yerusalemu ndisanabadwe ine; inde mtima wanga wapenyera kwambiri nzeru ndi chidziwitso.
171Ate. 5.21Ndipo ndinapereka mtima kudziwa nzeru ndi kudziwa misala ndi utsiru; ndinazindikira kuti ichinso chingosautsa mtima.
18Pakuti m'nzeru yambiri muli chisoni chambiri; ndi yemwe aenjezera chidziwitso aenjezera zowawa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.