MASALIMO 66 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Achenjeza onse alemekeze Mulungu pa ntchito zake zodabwitsaKwa Mkulu wa Nyimbo. Nyimbo, Salimo.

1 Mas. 100.1 Fuulirani kwa Mulungu, dziko lonse lapansi.

2Imbirani ulemerero wa dzina lake;

pomlemekeza mumchitire ulemerero.

3 Mas. 65.5 Nenani kwa Mulungu, Ha,

ntchito zanu nzoopsa nanga!

Chifukwa cha mphamvu yanu yaikulu adani anu adzagonjera Inu.

4 Mas. 22.27 Dziko lonse lapansi lidzakugwadirani,

ndipo lidzakuimbirani;

ndzaimbira dzina lanu.

5 Mas. 46.8 Idzani, muone ntchito za Mulungu;

zochitira Iye ana a anthu nzoopsa.

6 Eks. 14.21; Yos. 3.14, 16 Anasanduliza nyanja ikhale mtunda.

Anaoloka mtsinje choponda pansi,

apo tinakondwera mwa Iye.

7Achita ufumu mwa mphamvu yake kosatha;

maso ake ayang'anira amitundu;

opikisana ndi Iye asadzikuze.

8Lemekezani Mulungu wathu, mitundu ya anthu inu,

ndipo mumveketse liu la chilemekezo chake.

9 Mas. 121.3 Iye amene asunga moyo wathu tingafe,

osalola phazi lathu literereke.

10 Zek. 13.9 Pakuti munatiyesera, Mulungu,

munatiyenga monga ayenga siliva.

11Munapita nafe kuukonde;

munatisenza chothodwetsa pamsana pathu.

12 Yes. 43.2 Munapititsa anthu oberekeka pamwamba pamitu pathu;

tinapyola moto ndi madzi;

koma munatifikitsa potitsitsimutsa.

13Ndidzalowa m'nyumba yanu ndi nsembe zopsereza,

ndidzakuchitirani zowinda zanga,

14zimene inazitchula milomo yanga,

ndinazinena pakamwa panga posautsika ine.

15Ndidzakufukizirani nsembe zopsereza zonona,

pamodzi ndi chofukiza cha mphongo za nkhosa;

ndidzakonza ng'ombe pamodzi ndi mbuzi.

16 Mas. 34.11 Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu,

ndipo ndidzafotokozera zonse anazichitira moyo wanga.

17Ndinamfuulira Iye pakamwa panga,

ndipo ndinamkuza ndi lilime langa.

18 Miy. 28.9; Yoh. 9.31; Yak. 4.3 Ndikadasekera zopanda pake m'mtima mwanga,

Ambuye sakadamvera.

19 Mas. 116.1-2 Koma Mulungu anamvadi;

anamvera mau a pemphero langa.

20Wolemekezeka Mulungu,

amene sanandipatutsire ine pemphero langa,

kapena chifundo chake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help