2 MBIRI 36 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Yehowahazi, Yehoyakimu, Yehoyakini, mafumu a Yuda(2Maf. 23.30-35)

1 2Maf. 23.30-34 Pamenepo anthu a m'dziko anatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya, namlonga ufumu mu Yerusalemu, m'malo mwa atate wake.

2Yehowahazi anali wa zaka makumi awiri mphambu zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu miyezi itatu.

3Ndipo mfumu ya Aejipito anamchotsera ufumu wake mu Yerusalemu, nasonkhetsa dziko matalente zana limodzi a siliva, ndi talente limodzi la golide.

4Ndi mfumu ya Aejipito anamlonga Eliyakimu mng'ono wake mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu, nasintha dzina lake likhale Yehoyakimu. Koma Neko anatenga Yehowahazi mkulu wake, namuka naye ku Ejipito.

Yehoyakimu mfumu ya Yuda(2Maf. 23.36—24.7)

5 2Maf. 23.36-37 Yehoyakimu anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka khumi ndi chimodzi, nachita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wake.

62Maf. 24.1; Hab. 1.6Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anakwera kuyambana naye, nammanga ndi matangadza kumuka naye ku Babiloni.

72Maf. 24.13Nebukadinezara anatenganso ndi zipangizo za nyumba ya Yehova kunka nazo ku Babiloni, naziika mu Kachisi wake ku Babiloni.

82Maf. 24.5Machitidwe ena tsono a Yehoyakimu, ndi zonyansa zake anazichita, ndi zija zidapezeka zomtsutsa; taonani, zilembedwa m'buku la mafumu a Israele ndi Yuda; ndi Yehoyakini mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.

9 2Maf. 24.8-17 Yehoyakini anali wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu miyezi itatu, ndi masiku khumi; nachita choipa pamaso pa Yehova.

10Ndipo pofikanso nyengo, mfumu Nebukadinezara anatumiza anthu abwere naye ku Babiloni, pamodzi ndi zipangizo zokoma za nyumba ya Yehova; nalonga Zedekiya mbale wake mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu.

Zedekiya woipa, mfumu yotsiriza ya Yuda(2Maf. 24.18-20; Yer. 52.1-3a)

11 2Maf. 24.18-20; Yer. 52.1-3 Zedekiya anali wa zaka makumi awiri mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka khumi ndi chimodzi,

12nachita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wake; sanadzichepetse kwa Yeremiya mneneri wakunena zochokera pakamwa pa Yehova.

13Ndiponso anapandukana naye mfumu Nebukadinezara, amene adamlumbiritsa pa Mulungu; koma anaumitsa khosi lake, nalimbitsa mtima wake kusatembenukira kwa Yehova Mulungu wa Israele.

14Ndiponso ansembe aakulu onse ndi anthu anachulukitsa zolakwa zao, monga mwa zonyansa zonse za amitundu, nadetsa nyumba ya Yehova, imene anapatula mu Yerusalemu.

15Yer. 25.3Ndipo Yehova Mulungu wa makolo ao anatumiza kwa iwo ndi dzanja la mithenga yake, nalawirira mamawa kuituma, chifukwa anamvera chifundo anthu ake, ndi pokhala pake;

16Yer. 5.12-13; Mat. 23.34koma ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mau ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Yehova unaukira anthu ake, mpaka panalibe cholanditsa.

Yerusalemu apasulidwa anthu natengedwa ukapolo ku Babiloni(2Maf. 25.1-21; Yer. 52.3b-11)

17 2Maf. 25.1-15 Pakuti Iye anawakweretsera mfumu ya Ababiloni, ndiye anawaphera anyamata ao ndi lupanga, m'nyumba ya malo ao opatulika, osachitira chifundo mnyamata kapena namwali, mkulu kapena nkhalamba; Mulungu anawapereka onse m'dzanja lake.

18Ndi zipangizo zonse za nyumba ya Mulungu, zazikulu ndi zazing'ono, ndi chuma cha nyumba ya Yehova, ndi chuma cha mfumu, ndi cha akalonga ake, anabwera nazo zonsezi ku Babiloni.

19Ndipo anatentha nyumba ya Mulungu, nagumula linga la Yerusalemu, natentha nyumba zake zonse zachifumu ndi moto, naononga zipangizo zake zonse zokoma.

20Ndi iwo amene adapulumuka kulupanga anamuka nao ku Babiloni, nakhala iwo anyamata ake, ndi a ana ake, mpaka mfumu ya Persiya idachita ufumu;

21Lev. 26.34-35, 43; Yer. 25.9-12; 29.10; Dan. 9.2kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, mpaka dziko linakondwera nao masabata ake; masiku onse a kupasuka kwake linasunga Sabata, kukwaniritsa zaka makumi asanu ndi awiri.

Kirusi alola yense wofuna abwere kwao kukamanga Kachisi(Ezr. 1.1-4)

22 Ezr. 1.2-3; Yes. 44.28; Yer. 33.10-11, 14 Chaka choyamba tsono cha Kirusi mfumu ya Persiya, kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, Yehova anautsa mzimu wa Kirusi mfumu ya Persiya, kuti abukitse mau mu ufumu wake wonse, nawalembenso, ndi kuti,

23Atero Kirusi mfumu ya Persiya, Yehova Mulungu Wam'mwamba anandipatsa maufumu onse a padziko lapansi nandilangiza ndimmangire nyumba mu Yerusalemu, ndiwo ku Yuda. Aliyense mwa inu a anthu ake onse, Yehova Mulungu wake akhale naye, akwereko.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help