AHEBRI 3 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Khristu ali wamkulu woposa Mose. Awachenjeza amkhulupirire

1 Aro. 1.7; Aef. 4.1; Aheb. 4.14 Potero, abale oyera mtima, olandirana nao maitanidwe akumwamba, lingirirani za Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chivomerezo chathu, Yesu;

2Num. 12.7amene anakhala wokhulupirika kwa Iye adamuikayo, monganso Mose m'nyumba yake yonse.

3Pakuti ameneyo wayesedwa woyenera ulemerero woposa Mose, monga momwe iye amene anaimanga nyumba ali nao ulemerero woposa nyumbayi.

4Aef. 2.10Pakuti nyumba iliyonse ili naye wina woimanga; koma wozimanga zonse ndiye Mulungu.

5Aheb. 3.2; Deut. 18.15, 18-19Ndipo Mosetu anali wokhulupirika m'nyumba yake yonse, monga mnyamata, achitire umboni izi zidzalankhulidwazi;

6Aheb. 1.2; Aef. 2.21-22koma Khristu monga mwana, wosunga nyumba yake; ndife nyumba yake, ngati tigwiritsa kulimbika mtima ndi kudzitamandira kwa chiyembekezocho, kuchigwira kufikira chitsiriziro.

7Mas. 95.7, 11Momwemo, monga anena Mzimu Woyera,

Lero ngati mudzamva mau ake,

8musaumitse mitima yanu, monga m'kupsetsa mtimamo,

monga muja tsiku la chiyesero m'chipululu,

9chimene makolo anu anandiyesa nacho,

ndi kundivomereza,

naona ntchito zanga zaka makumi anai.

10Momwemo ndinakwiya nao mbadwo uwu,

ndipo ndinati, Nthawi zonse amasochera mumtima;

koma sanazindikire njira zanga iwowa;

11Monga ndinalumbira mu ukali wanga:

Ngati adzalowa mpumulo wanga!

12Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;

13komatu dandaulirananani nokha tsiku ndi tsiku, pamene patchedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjerero la uchimo;

14Aheb. 3.6pakuti takhala ife olandirana ndi Khristu, ngatitu tigwiritsa chiyambi cha kutama kwathu kuchigwira kufikira chitsiriziro;

15Aheb. 3.7umo anenamo,

Lero ngati mudzamva mau ake,

musaumitse mitima yanu, monga pa kupsetsa mtima.

16 Num. 14.2, 4, 11, 24, 29-30 Pakuti ndi ayani, pakumva, anapsetsa mtima? Kodi si onse aja adatuluka mu Ejipito ndi Mose?

17Num. 14.22, 29Koma anakwiya ndi ayani zaka makumi anai? Kodi si ndi awo adachimwawo, amene matupi ao adagwa m'chipululu?

18Num. 14.30Ndipo adawalumbirira ayani kuti asalowe mpumulo wake?

19Mas. 78.22; Aheb. 4.6Si awo kodi osamverawo? Ndipo tiona kuti sanathe kulowa chifukwa cha kusakhulupirira.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help