YESAYA 35 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Chikondwerero cha Ziyoni m'tsogolomo

1 Mas. 72.16 Chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti see lidzasangalala ndi kuphuka ngati duwa.

2Yes. 40.5; Zef. 1.7Lidzaphuka mochuluka ndi kusangalala, ngakhale kukondwa ndi kuimba; lidzapatsidwa ulemerero wa Lebanoni, ndi ukulu wa Karimele ndi Saroni; anthuwo adzaona ulemerero wa Yehova, ukulu wake wa Mulungu wathu.

3 Aheb. 12.12-13 Limbitsani manja opanda mphamvu, ndi kulimbitsa maondo a gwedegwede.

4Nenani kwa a mitima ya chinthenthe, Limbani, musaope; taonani, Mulungu wanu adza ndi kubwezera chilango, ndi mphotho ya Mulungu; Iye adzafika ndi kukupulumutsani.

5Mrk. 7.32-35; Yoh. 9.6-7Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa.

6Mat. 9.32-33; Yoh. 7.38-39; Mac. 3.2Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba; pakuti m'chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m'dziko loti see.

7Ndipo mchenga wong'azimira udzasanduka thamanda, ndi nthaka yopanda madzi idzasanduka zitsime zamadzi; m'malo a ankhandwe m'mene iwo anagona, mudzakhala udzu ndi mabango ndi milulu.

8Yow. 3.17Ndipo kudzakhala khwalala kumeneko, ndi njira, ndipo idzatchedwa njira yopatulika; odetsedwa sadzapita m'menemo; koma Iye adzakhala nao oyenda m'njira, ngakhale opusa, sadzasochera m'menemo.

9Ezk. 34.25Sikudzakhala mkango kumeneko, ngakhale chilombo cholusa sichidzapondapo, pena kupezedwa pamenepo; koma akuomboledwa adzayenda m'menemo;

10Yes. 51.11; Chiv. 7.17; 21.4ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni alikuimba; kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; iwo adzakhala ndi kusekerera ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help