1 Mas. 106.1 Yamikani Yehova pakuti ndiye wabwino;
pakuti chifundo chake nchosatha.
2Yamikani Mulungu wa milungu;
pakuti chifundo chake nchosatha.
3Yamikani Mbuye wa ambuye;
pakuti chifundo chake nchosatha.
4 Mas. 72.18 Amene yekha achita zodabwitsa zazikulu;
pakuti chifundo chake nchosatha.
5 Yer. 51.15 Amene analenga zakumwamba mwanzeru;
pakuti chifundo chake nchosatha.
6Amene anayala dziko lapansi pamwamba pamadzi;
pakuti chifundo chake nchosatha.
7 Gen. 1.14, 16 Amene analenga miuni yaikulu;
pakuti chifundo chake nchosatha.
8Dzuwa liweruze usana;
pakuti chifundo chake nchosatha.
9Mwezi ndi nyenyezi ziweruze usiku;
pakuti chifundo chake nchosatha.
10 Eks. 12.29 Iye amene anapandira Aejipito ana ao oyamba;
pakuti chifundo chake nchosatha.
11Natulutsa Israele pakati pao;
pakuti chifundo chake nchosatha.
12Ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka;
pakuti chifundo chake nchosatha.
13 Eks. 14.21-22 Amene anagawa magawo Nyanja Yofiira;
pakuti chifundo chake nchosatha.
14Napititsa Israele pakati pake;
pakuti chifundo chake nchosatha.
15 Eks. 14.27 Nakhuthula Farao ndi khamu lake mu Nyanja Yofiira:
pakuti chifundo chake nchosatha.
16 Eks. 15.22 Amene anatsogolera anthu ake m'chipululu;
pakuti chifundo chake nchosatha.
17 Deut. 29.7 Amene anapanda mafumu aakulu;
pakuti chifundo chake nchosatha.
18Ndipo anawapha mafumu omveka;
pakuti chifundo chake nchosatha.
19Sihoni mfumu ya Aamori;
pakuti chifundo chake nchosatha.
20Ndi Ogi mfumu ya Basani;
pakuti chifundo chake nchosatha.
21 Yos. 12 Ndipo anapereka dziko lao likhale cholowa;
pakuti chifundo chake nchosatha.
22Cholowa cha kwa Israele mtumiki wake;
pakuti chifundo chake nchosatha.
23Amene anatikumbukira popepuka ife;
pakuti chifundo chake nchosatha.
24Natikwatula kwa otisautsa;
pakuti chifundo chake nchosatha.
25 Mas. 104.27 Ndiye wakupatsa nyama zonse chakudya;
pakuti chifundo chake nchosatha.
26Yamikani Mulungu wa Kumwamba,
pakuti chifundo chake nchosatha.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.