1Ndipo akulu a makolo a mabanja a ana a Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, wa mabanja a ana a Yosefe, anayandikiza, nanena pamaso pa Mose, ndi pamaso pa akalonga, ndiwo akulu a makolo a ana a Israele;
2Num. 27nati, Yehova analamulira mbuye wanga mupatse ana a Israele dzikoli mochita maere likhale cholowa chao; ndipo Yehova analamulira mbuye wathu mupatse ana ake aakazi cholowa cha Zelofehadi mbale wathu.
3Ndipo akakwatibwa nao ana aamuna a mafuko ena a ana a Israele, achichotse cholowa chao ku cholowa cha makolo athu, nachionjeze ku cholowa cha fuko limene adzakhalako; chotero achichotse ku maere a cholowa chathu.
4Lev. 25.10Ndipo pofika chaka choliza cha ana a Israele adzaphatikiza cholowa chao ku cholowa cha fuko limene akhalako; chotero adzachotsa cholowa chao ku cholowa cha fuko la makolo athu.
5Ndipo Mose analamulira ana a Israele monga mwa mau a Yehova, nati, Fuko la ana a Yosefe linena zoona.
6Cholamulira Yehova za ana aakazi a Zelofehadi ndi ichi, kuti, Akwatibwe nao amene afuna eni ake; komatu akwatibwe nao a banja la fuko la makolo ao okhaokha.
71Maf. 21.3Motero cholowa cha ana a Israele sichidzanka ku fuko ndi fuko; popeza ana a Israele adzamamatira yense ku cholowa cha fuko la makolo ake.
81Mbi. 23.22Ndipo mwana wamkazi yense wa mafuko a ana a Israele, wakukhala nacho cholowa, akwatibwe ndi wina wa banja la fuko la kholo lake, kuti ana a Israele akhale nacho yense cholowa cha makolo ake.
9Motero cholowa cha ana a Israele sichidzanka ku fuko ndi fuko, pakuti mafuko a ana a Israele adzamamatira lonse ku cholowa chakechake.
10Monga Yehova adalamulira Mose, momwemo ana aakazi a Zelofehadi anachita;
11popeza Mala, Tiriza, ndi Hogila, ndi Milika, ndi Nowa, ana aakazi a Zelofehadi, anakwatibwa ndi ana aamuna a abale a atate wao.
12Anakwatibwa mwa mabanja a ana a Manase mwana wa Yosefe; ndipo cholowa chao chinakhala m'fuko la banja la atate wao.
13Awa ndi malamulo ndi maweruzo, amene Yehova analamulira ana a Israele ndi dzanja la Mose m'zidikha za Mowabu pa Yordani ku Yeriko.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.