MIKA Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mau OyambaMneneriyu adalalika mau ake ku Yuda panthawi ya mneneri Yesaya. Iye ankadziwiratu kuti ufumu wa Yuda nawonso udzawonongedwa. Monga muja Yehova adalangira ufumu wakumpoto chifukwa Aisraelewo ntchito zao zinali zopanda chilungamo, momwemonso adzalanga ndi Ayuda omwe chifukwa cha zochita zao zosalungama. Komabe pa mau ake Mika akuonetsa chikhulupiriro chakuti Mulungu adzakonzanso zinthu kutsogoloko kuti zidzakhale bwino.Kutsogoloko Mulungu adzakhazikitsanso ufumu wake kudzera mwa mmodzi mwa zidzukulu za Davide, ndipo adzadzetsa mtendere ponseponse (5.2-4).Mau ena ofunikira kwambiri amene akunena mwachidule zimene aneneri anali kulalikira ndi awa akuti, “Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.” (6.8)Za mkatimuMau a Yehova otsutsa Aisraele ndi Ayuda 1.1—3.12

Mau ena a Yehova olonjeza zabwino 4.1—5.15

Mau ena a Yehova ochenjeza anthu, mau ena otsutsa chikhulupiriro 6.1—7.20

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help