1Akapeza munthu waphedwa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanulanu, nagona pamunda, wosadziwika wakumkantha,
2pamenepo azituluka akulu anu ndi oweruza anu, nayese kumizinda yomzinga wophedwayo;
3ndipo kudzali kuti mzinda wakukhala kufupi kwa munthu wophedwayo, inde akulu a mzinda uwu atenge ng'ombe yaikazi yosagwira ntchito, yosakoka goli;
4ndipo akulu a mzinda uwu atsike nayo ng'ombeyo ku chigwa choyendako madzi, chosalima ndi chosabzala, nayidula khosi ng'ombeyo m'chigwamo;
5ndipo ansembe, ana a Levi, ayandikize; pakuti Yehova Mulungu wanu anasankha iwo kumtumikira ndi kudalitsa m'dzina la Yehova; ndipo kutengana konse ndi kupandana konse kukonzeke monga mwa mau awa.
6Mas. 26.6; Mat. 27.24Ndipo akulu onse a mzindawo wokhala pafupi pa munthu wophedwayo azisamba manja ao pa ng'ombeyo yodulidwa khosi m'chigwamo;
7nayankhe nati, Manja athu sanakhetse mwazi uwu, ndi maso athu sanauone.
8Yon. 1.14Landirani, Yehova, chotetezera anthu anu Israele, amene munawaombola, ndipo musalole mwazi wosachimwa ukhale pakati pa anthu anu Israele; ndipo adzawatetezera cha mwaziwo.
9Chotero mudzichotsere mwazi wosachimwa pakati panu, pakuti wachita choyenera pamaso pa Yehova.
Za akazi otengedwa kunkhondo10Pamene mutuluka kunka ku nkhondo ya pa adani anu, ndipo Yehova Mulungu wanu awapereka m'manja mwanu, ndipo muwagwira akhale akapolo anu;
11mukaona mwa akapolowa mkazi wokongola, mukamkhumba, ndi kufuna mumtenga akhale mkazi wanu;
12pamenepo mufike naye kwanu kunyumba yanu; ndipo amete tsitsi la pamutu pake, ndi kuwenga makadabo ake;
13navule zovala za ukapolo wake, nakhale m'nyumba mwanu, nalire atate wake, ndi mai wake mwezi wamphumphu; ndipo atatero mulowe naye ndi kukhala mwamuna wake, ndi iye akhale mkazi wanu.
14Ndipo kudzali, mukapanda kukondwera naye, mumlole apite komwe afuna; koma musamgulitsa ndalama konse, musamamuyesa chuma, popeza wamchepetsa.
Mphamvu ya oyamba kubadwa15Munthu akakhala nao akazi awiri, wina wokondana naye, wina wodana naye, nakambalira ana, wokondana naye, ndi wodana naye yemwe; ndipo mwana wamwamuna woyamba akakhala wa iye uja anadana naye;
16pamenepo kudzali, tsiku lakugawira ana ake aamuna chuma chake, sangakhoze kuyesa mwana wa wokondana naye woyamba kubadwa, wosati mwana wa wodana naye, ndiye woyamba kubadwatu.
17Koma azivomereza wobadwa woyamba, mwana wa wodana naye, ndi kumwirikizira gawo lake la zake zonse; popeza iye ndiye chiyambi cha mphamvu yake; zoyenera woyamba kubadwa nzake.
Za ana opulukira osamvera18Munthu akakhala naye mwana wamwamuna wopulukira, ndi wopikisana naye, wosamvera mau a atate wake, kapena mau a mai wake, wosawamvera angakhale anamlanga;
19azimgwira atate wake ndi mai wake, ndi kutulukira naye kwa akulu a mzinda wake, ndi ku chipata cha malo ake;
20ndipo anene kwa akulu a mzinda wake, Mwana wathu wamwamuna uyu ngwopulukira ndi wopikisana nafe, wosamvera mau athu, ndiye womwazamwaza, ndi woledzera.
21Pamenepo amuna onse a mzinda wake amponye miyala kuti afe; chotero muchotse choipacho pakati panu; ndipo Israele wonse adzamva, nadzaopa.
Za kuika wophedwa mompachika22Munthu akakhala nalo tchimo loyenera imfa, kuti amuphe, ndipo wampachika;
23Yos. 8.29; Yoh. 19.31; Agal. 3.13mtembo wake usakhale pamtengo usiku wonse, koma mumuike ndithu tsiku lomwelo; pakuti wopachikidwa pamtengo atembereredwa ndi Mulungu; kuti mungadetse dziko lanu limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.