1Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha, nati,
2Kulamulira ndi kuopsa kuli ndi Iye;
achita mtendere pa zam'mwamba zake.
3 Yak. 1.17 Ngati awerengedwa makamu ake?
Ndipo ndaniyo, kuunika kwake sikumtulukira?
4 Mas. 130.3-4 Potero munthu akhala bwanji wolungama kwa Mulungu?
Kapena wobadwa ndi mkazi akhala woyera bwanji?
5Taonani, ngakhale mwezi ulibe kuwala;
ndi nyenyezi siziyera pamaso pake;
6 Mas. 22.6 kopambana kotani nanga munthu, ndiye mphutsi!
Ndi wobadwa ndi munthu, ndiye nyongolotsi!
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.