YOBU 20 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Zofari afotokozera masautso amene Mulungu atumizira oipa

1Pamenepo anayankha Zofari Mnaama, nati,

2M'mwemo zolingirira zanga zindiyankha,

chifukwa chake ndifulumidwa m'kati mwanga.

3Ndamva kudzudzula kwakundichititsa manyazi,

ndi mzimu wa nzeru yanga undiyankha.

4Kodi suchidziwa ichi chiyambire kale lomwe,

kuyambira anaika munthu padziko lapansi,

5 Mas. 37.35-36 kuti kufuula kokondwera kwa woipa sikukhalira kutha,

ndi chimwemwe cha wonyoza Mulungu chikhala kamphindi?

6 Yes. 14.13-14 Chinkana ukulu wake ukwera kunka kuthambo,

nugunda pamitambo mutu wake;

7koma adzatayika kosatha ngati zonyansa zake;

iwo amene adamuona adzati, Ali kuti iye?

8 Mas. 73.20 Adzauluka ngati loto, osapezekanso;

nadzaingidwa ngati masomphenya a usiku.

9Diso lidamuonalo silidzamuonanso;

ndi malo ake sadzampenyanso.

10Ana ake adzapempha aumphawi awakomere mtima;

ndi manja ake adzabweza chuma chake.

11 Mas. 25.7 Mafupa ake adzala nao unyamata wake,

koma udzagona naye pansi m'fumbi.

12Chinkana choipa chizuna m'kamwa mwake,

chinkana achibisa pansi pa lilime lake;

13chinkana achisunga, osachileka,

nachikhalitsa m'kamwa mwake;

14koma chakudya chake chidzasandulika m'matumbo mwake,

chidzakhala ndulu ya mphiri m'kati mwake.

15Anachimeza chuma koma adzachisanzanso;

Mulungu adzachitulutsa m'mimba mwake.

16Adzayamwa ndulu ya mphiri;

pakamwa pa njoka padzamupha.

17Sadzapenyerera timitsinje,

toyenda nao uchi ndi mafuta.

18Chimene adagwiriracho ntchito, adzachibweza, osachimeza;

sadzakondwera monga mwa zolemera zake adaziona.

19Pakuti anapsinja, nasiya aumphawi;

analanda nyumba mwachiwawa, imene sanaimange.

20 Mlal. 5.13 Popeza sanadziwe kupumula m'kati mwake,

sadzalanditsa kanthu ka zofunika zake.

21Sikunatsalira kanthu kosadya iye,

chifukwa chake zokoma zake sizidzakhalitsa.

22Pomkwanira kudzala kwake adzakhala m'kusauka;

dzanja la yense wovutika lidzamgwera.

23 Num. 11.33 Poti adzaze mimba yake,

Mulungu adzamponyera mkwiyo wake waukali,

nadzamvumbitsira uwu pakudya iye.

24Adzathawa chida chachitsulo,

ndi muvi wa uta wamkuwa udzampyoza.

25Auzula, nutuluka m'thupi mwake;

inde nsonga yonyezimira ituluka m'ndulu mwake;

zamgwera zoopsa.

26 Mas. 21.9 Zamdima zonse zimsungikira zikhale chuma chake,

moto wosaukoleza munthu udzampsereza;

udzatha wotsalira m'hema mwake.

27M'mwamba mudzavumbulutsa mphulupulu yake,

ndi dziko lapansi lidzamuukira.

28Phindu la m'nyumba mwake lidzachoka,

akatundu ake adzamthawa tsiku la mkwiyo wake.

29Ili ndi gawo la munthu woipa, lochokera kwa Mulungu,

ndi cholowa amuikiratu Mulungu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help