1 1Ate. 4.16 Ndipo tikupemphani, abale, chifukwa cha kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi kusonkhana pamodzi kwathu kwa Iye;
2Mat. 24.4-5kuti musamagwedezeka mtima msanga ndi kutaya maganizo anu, kapena kuopsedwa, mwa mzimu kapena mwa mau; kapena mwa kalata, monga wolembedwa ndi ife, monga ngati tsiku la Ambuye lafika;
3Mat. 24.4-5; 1Tim. 4.1; 1Yoh. 2.18munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika, koma chiyambe chafika chipatukocho, navumbulutsike munthu wosaweruzika, mwana wa chionongeko,
4Yes. 14.13-14amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zotchedwa Mulungu, kapena zopembedzeka; kotero kuti iye wakhala pansi ku Kachisi wa Mulungu, nadzionetsera yekha kuti ali Mulungu.
5Simukumbukira kodi, kuti pokhala nanu, ndisanachoke ine, ndinakuuzani izi?
6Ndipo tsopano chomletsa muchidziwa, kuti akavumbulitsidwe iye m'nyengo yake ya iye yekha.
71Yoh. 2.18Pakuti chinsinsi cha kusaweruzika chayambadi kuchita; chokhachi pali womletsa tsopano, kufikira akamchotsa pakati.
8Chiv. 19.20-21Ndipo pamenepo adzavumbulutsidwa wosaweruzikayo, amene Ambuye Yesu adzamthera ndi mzimu wa pakamwa pake, nadzamuononga ndi maonekedwe a kudza kwake;
9Mat. 24.24; Aef. 2.2ndiye amene kudza kwake kuli monga mwa machitidwe a Satana, mu mphamvu yonse, ndi zizindikiro ndi zozizwa zonama;
10ndi m'chinyengo chonse cha chosalungama kwa iwo akuonongeka, popeza chikondi cha choonadi sanachilandire, kuti akapulumutsidwe iwo.
11Aro. 1.24-32Ndipo chifukwa chake Mulungu atumiza kwa iwo machitidwe a kusocheretsa, kuti akhulupirire bodza;
12Aro. 1.24-32kuti aweruzidwe onse amene sanakhulupirire choonadi, komatu anakondwera ndi chosalungama.
13 2Ate. 1.3 Koma tiyenera ife tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale okondedwa ndi Ambuye, kuti Mulungu anakusankhani inu kuyambira pachiyambi, mulandire chipulumutso mwa chiyeretso cha Mzimu ndi chikhulupiriro cha choonadi;
14Yoh. 17.22kumene anaitanako inu mwa Uthenga Wabwino wathu, kuti mulandire ulemerero wa Ambuye wathu Yesu Khristu.
15Afi. 4.1Chifukwa chake tsono, abale, chilimikani, gwiritsani miyambo imene tinakuphunzitsani, kapena mwa mau, kapena mwa kalata yathu.
16 1Yoh. 4.10 Ndipo Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate wathu amene anatikonda natipatsa chisangalatso chosatha ndi chiyembekezo chokoma mwa chisomo,
171Pet. 5.10asangalatse mitima yanu, nakhazikitse inu mu ntchito yonse ndi mau onse abwino.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.