MALIRO 4 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Tsoka la anthu Ayuda

1Ha! Golide wagugadi; golide woona woposa wasandulika;

miyala ya malo opatulika yakhuthulidwa

pa malekezero a makwalala onse.

2Ana a Ziyoni a mtengo wapatali,

olingana ndi golide woyengetsa,

angoyesedwa ngati mbiya zadothi zozipanga manja a woumba.

3Angakhale ankhandwe amapatsa bere, nayamwitsa ana ao;

koma mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga

wasanduka wankhanza,

ngati nthiwatiwa za m'chipululu.

4 Mali. 2.11-12 Lilime la mwana woyamwa limamatira

kumalakalaka kwake ndi ludzu;

ana aang'ono apempha mkate koma palibe wakuwanyemera.

5Omwe anadya zolongosoka angosiyidwa m'makwalala;

omwe analeredwa navekedwa mlangali afungatira madzala.

6 Gen. 19.25; Mat. 10.15 Pakuti mphulupulu ya mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga,

ikula koposa tchimo la Sodomu,

umene unapasuka m'kamphindi, anthu osauchitira kanthu.

7Omveka ake anakonzeka

koposa chipale chofewa, nayera koposa mkaka,

matupi ao anafiira koposa timiyala toti psu;

maonekedwe ao ananga a safiro wa mtengo wapatali.

8Maonekedwe ao ada koposa makala,

sazindikirika m'makwalala;

khungu lao limamatira pa mafupa ao,

lakhwinyata, lasanduka ngati ndodo.

9Ophedwa ndi lupanga amva bwino

kupambana ophedwa ndi njala;

pakuti amenewa angokwalika napyozedwa,

posowa zipatso za m'munda.

10 2Maf. 6.29 Manja a akazi achisoni anaphika ana aoao;

anali chakudya chao poonongeka

mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga.

11Yehova wakwaniritsa kuzaza kwake, watsanulira ukali wake;

anayatsa moto mu Ziyoni, unanyambita maziko ake.

12Mafumu a dziko lapansi sanakhulupirire,

ngakhale onse okhala kunja kuno,

kuti adani ndi amaliwongo adzalowadi m'zipata za Yerusalemu.

13 Ezk. 22.26, 28; Mat. 23.31, 37 Ndicho chifukwa cha machimo a aneneri

ndi mphulupulu za ansembe ake,

amene anakhetsa mwazi wa olungama pakati pake.

14 Num. 19.16; Yer. 2.34 Asochera m'makwalala ngati akhungu,

aipsidwa ndi mwazi;

anthu sangakhudze zovala zao.

15Amafuula kwa iwo, Chokani, osakonzeka inu,

chokani, chokani, musakhudze kanthu.

Pothawa iwo ndi kusochera,

anthu anati kwa amitundu,

Sadzagoneranso kuno.

16Mkwiyo wa Yehova unawalekanitsa, sadzawasamaliranso;

iwo sanalemekeze ansembe, sanakomere mtima akulu.

17 2Maf. 24.7 Maso athu athedwa, tikali ndi moyo,

poyembekeza thandizo chabe;

kudikira tinadikira mtundu wosatha kupulumutsa.

18 2Maf. 25.4-5 Amalondola mapazi athu, sitingayende m'makwalala athu;

chitsiriziro chathu chayandikira, masiku athu akwaniridwa;

pakuti chitsiriziro chathu chafikadi.

19 Deut. 28.49 Otilondola anaposa ziombankhanga

za m'mlengalenga m'liwiro lao,

anatithamangitsa pamapiri natilalira m'chipululu.

20 Yer. 52.9 Wodzozedwa wa Yehova,

ndiye mpweya wa m'mphuno mwathu,

anagwidwa m'maenje ao;

amene tinanena kuti,

Tidzakhala m'mthunzi mwake pakati pa amitundu,

21 Oba. 10 kondwera nusangalale, mwana wamkazi wa Edomu,

wokhala m'dziko la Uzi;

chikho chidzapita ngakhale mwa iwenso;

udzaledzera ndi kuvula zako.

22 Mas. 137.7; Yes. 40.2 Mphulupulu yako yatha, mwana wamkazi wa Ziyoni,

Yehova sadzakutenganso ndende;

koma adzazonda mphulupulu yako, mwana wa mkazi wa Edomu,

nadzavumbulutsa zochimwa zako.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help