1Mau a Yehova a kwa Yowele mwana wa Petuwele.
2Imvani ichi, akuluakulu inu, nimutchere khutu, inu nonse okhala m'dziko. Chachitika ichi masiku anu kodi, kapena masiku a makolo anu?
3Mas. 78.4Mufotokozere ana anu ichi, ndi ana anu afotokozere ana ao, ndi ana ao afotokozere mbadwo wina.
4Deut. 28.38Chosiya chimbalanga, dzombe lidachidya; ndi chosiya dzombe, chirimamine adachidya; ndi chosiya chirimamine, anoni adachidya.
5Galamukani, oledzera inu, nimulire; bumani, nonse akumwa vinyo, chifukwa cha vinyo watsopano; pakuti waletsedwa pakamwa panu.
6Miy. 30.25-27Pakuti mtundu wadza, wakwerera dziko langa, wamphamvu wosawerengeka, mano ake akunga mano a mkango, nukhala nao mano a chibwano a mkango waukulu.
7Yes. 5.5-7Unaonongadi mpesa wanga, nunyenya mkuyu wanga, nukungudza konse, nuutaya; nthambi zake zasanduka zotumbuluka.
8Lirani ngati namwali wodzimangira m'chuuno chiguduli, chifukwa cha mwamuna wa unamwali wake.
9Nsembe yaufa ndi nsembe yothira zalekeka kunyumba ya Yehova; ansembe, atumiki a Yehova, achita maliro.
10Yer. 12.11M'munda mwaonongeka, nthaka ilira; pakuti tirigu waonongeka, vinyo watsopano wamwelera, mafuta akudza pang'onong'ono.
11Gomani, akulima m'minda inu; lirani, akulima mpesa; chifukwa cha tirigu ndi barele; pakuti dzinthu za m'minda zatayika.
12Mpesa wauma, mkuyu wafota, mtengo wa mkangaza ndi kanjedza ndi muula, inde mitengo yonse yakuthengo yafota; pakuti chimwemwe chathera ana a anthu.
13Yer. 4.8Mudzimangire chiguduli m'chuuno mwanu, nimulire, ansembe inu; bumani otumikira kuguwa la nsembe inu; lowani, gonani usiku wonse m'chiguduli, inu otumikira Mulungu wanga; pakuti nsembe yaufa ndi nsembe yothira zaletsedwera nyumba ya Mulungu wanu.
142Mbi. 20.3-4, 13Patulani tsiku losala, lalikirani misonkhano yoletsa, sonkhanitsani akuluakulu, ndi onse okhala m'dziko, kunyumba ya Yehova Mulungu wanu; nimufuulire kwa Yehova.
15Yes. 13.6-9Kalanga ine, tsikuli! Pakuti layandikira tsiku la Yehova, lidzafika ngati chionongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse.
16Chakudya sichichotsedwa kodi pamaso pathu? Chimwemwe ndi chikondwerero pa nyumba ya Mulungu wathu?
17Mbeu zaola pansi pa zibuluma zao; zosungiramo zaonongeka, nkhokwe zapasuka; pakuti tirigu wakwinyata.
18Ha! Nyama ziusa moyo, magulu a ng'ombe azimidwa; pakuti zisowa podyera; magulu a nkhosa omwe atha.
19Mas. 50.15Ndifuulira kwa Inu Yehova, pakuti moto wapsereza mabusa a m'chipululu, ndi malawi a moto anatentha mitengo yonse yakuthengo.
20Mas. 104.21; 145.15Inde nyama zakuthengo zilira kwa Inu; pakuti mitsinje yamadzi yaphwa, ndi moto wapsereza mabusa a m'chipululu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.