MASALIMO 112 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Adalitsidwa akuopa Mulungu

1 Mas. 128.1; 119.16, 47 Aleluya.

Wodala munthu wakuopa Yehova,

wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake.

2 Mas. 25.13 Mbeu yake idzakhala yamphamvu padziko lapansi;

mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa.

3 Mat. 6.33 M'nyumba mwake mudzakhala akatundu ndi chuma:

Ndi chilungamo chake chikhala chikhalire.

4 Mas. 97.11 Kuunika kutulukira oongoka mtima mumdima;

Iye ndiye wachisomo, ndi wansoni ndi wolungama.

5 Luk. 6.35 Wodala munthu wakuchitira chifundo, nakongoletsa;

adzalimbika nao mlandu wake poweruzidwa.

6 Miy. 10.7 Popeza sadzagwedezeka nthawi zonse;

wolungama adzakumbukika ku nthawi yosatha.

7 Miy. 1.33 Sadzaopa mbiri yoipa;

mtima wake ngwokhazikika, wokhulupirira Yehova.

8Mtima wake ngwochirikizika, sadzachita mantha,

kufikira ataona chofuna iye pa iwo omsautsa.

9 2Ako. 9.9 Anagawagawa, anapatsa aumphawi;

chilungamo chake chikhalitsa kosatha;

nyanga yake idzakwezeka ndi ulemu.

10 Miy. 10.28; Luk. 13.28 Woipa adzaziona, nadzapsa mtima;

adzakukuta mano, nadzasungunuka;

chokhumba oipa chidzatayika.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help