TITO Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mau OyambaTito sanali Myuda koma wa mitundu ina. Atatembenuka ndi kulowa mu mpingo, adasanduka mnzake wa Paulo womthandiza pa ntchito yolalikira, namuperekeza pa maulendo ake. Paulo adamsiya ku chilumba cha Krete kuti aziyang'anira mpingo kumeneko.Pomulembera kalatayi, Paulo akumukumbutsa za makhalidwe oyenera atsogoleri a mpingo, makamaka ku Krete poti anthuwo mbiri yao sinali yabwino. Kenaka akumufotokozera kuti iye ayenera kuphunzitsira magulu ena a Akhristu: azibambo okalamba, amai okalamba (kuti iwonso aziphunzitsa amai achitsikana), achinyamata ndipo akapolo. Potsiriza Paulo alangiza Tito pa za mayendedwe a Chikhristu, kuti adziwe kuyanjanitsa anthu ndi kukopa mitima yao, apewe zilizonse zimene zingabweretse kukangana kapena kupatukana mu mpingo.Za mkatimuMau oyamba 1.1-4Za atsogoleri a mpingo 1.5-16Ntchito yosamalira magulu osiyanasiyana mu mpingo 2.1-15Malangizo ndi mau ena ochenjeza 3.1-11Mau omaliza 3.12-15
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help