YEREMIYA 31 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mwa chikondi cha Mulungu adzabweza Israele

1Nthawi yomweyo, ati Yehova, ndidzakhala Mulungu wa mabanja onse a Israele, ndipo iwo adzakhala anthu anga.

2Num. 10.33Atero Yehova, Anthu opulumuka m'lupanga anapeza chisomo m'chipululu; Israele, muja anakapuma.

3Hos. 1.4; Mala. 1.2; Aro. 11.28-29Yehova anaonekera kwa ine kale, ndi kuti, Inde, ndakukonda iwe ndi chikondi chosatha; chifukwa chake ndakukoka iwe ndi kukukomera mtima.

4Ndidzamangitsanso mudzi wako, ndipo udzamangidwa, iwe namwali wa Israele; udzakometsedwanso ndi mangaka, ndipo udzatulukira masewero a iwo akukondwerera.

5Yes. 65.21Ndiponso udzalima minda ya mpesa pa mapiri a Samariya; akuoka adzaoka, nadzayesa zipatso zake zosapatulidwa.

6Mik. 4.2Pakuti lidzafika tsiku, limene alonda a pa mapiri a Efuremu adzafuula, Ukani inu, tikwere ku Ziyoni kwa Yehova Mulungu wathu.

7Yes. 12.5-6Pakuti Yehova atero, Imbirani Yakobo ndi kukondwa, fuulirani mtundu woposawo; lalikirani, yamikirani, ndi kuti, Yehova, mupulumutse anthu anu, ndi otsala a Israele.

8Yer. 3.12, 18Taonani, ndidzatenga iwo kudziko la kumpoto, ndidzasonkhanitsa iwo ku malekezero a dziko lapansi, pamodzi ndi osaona ndi opunduka mwendo, mkazi amene ali ndi pakati ndi mkazi alinkubala pamodzi; khamu lalikulu lidzabwera kuno.

9Eks. 4.22; Mas. 126.5-6Adzadza ndi kulira, ndipo ndidzawatsogolera ndi mapembedzero, ndidzawayendetsa kumitsinje yamadzi, m'njira yoongoka m'mene sadzaphunthwa, pakuti ndili Atate wake wa Israele, ndipo Efuremu ali mwana wanga woyamba.

10 Ezk. 34.12-15 Tamvani mau a Yehova, amitundu inu, lalikirani m'zisumbu zakutali; ndi kuti, Iye amene anabalalitsa Israele adzasonkhanitsa, nadzamsunga, monga mbusa achita ndi zoweta zake.

11Yes. 48.20Pakuti Yehova wapulumutsa Yakobo, namuombola iye m'dzanja la iye amene anamposa mphamvu.

12Yes. 58.11; Hos. 3.5Ndipo adzadza nadzaimba pa msanje wa Ziyoni, nadzasonkhanira ku zokoma za Yehova, kutirigu, ndi kuvinyo, ndi mafuta, ndi kwa ana a zoweta zazing'ono ndi zazikulu; ndipo moyo wao udzakhala ngati munda wamichera; ndipo sadzakhalanso konse ndi chisoni.

13Ndipo namwali adzasangalala m'masewero, ndi anyamata ndi nkhalamba pamodzi; pakuti ndidzasandutsa kulira kwao kukhale kukondwera, ndipo ndidzatonthoza mitima yao, ndi kuwasangalatsa iwo asiye chisoni chao.

14Ndipo ndikhutitsa moyo wa ansembe ndi mafuta, ndipo anthu anga adzakhuta ndi zokoma zanga, ati Yehova.

Rakele adzatonthozedwa

15 Mat. 2.17-18 Atero Yehova: Mau a amveka mu Rama, maliro ndi kulira kwakuwawa, Rakele alinkulirira ana ake; akana kutonthozedwa mtima pa ana ake, chifukwa palibe iwo.

16Yehova atero: Letsa mau ako asalire, ndi maso anu asagwe misozi; pakuti ntchito yako idzalandira mphotho, ati Yehova; ndipo adzabweranso kuchokera kudziko la mdani.

17Ndipo chilipo chiyembekezero cha chitsirizo chako, ati Yehova; ndipo ana ako adzafikanso ku malire ao.

18Mali. 5.21Kumva ndamva Efuremu alinkulirira kotero, Mwandilanga ine, ndipo ndalangidwa, monga mwanawang'ombe wosazolowera goli; munditembenuze ine, ndipo ine ndidzatembenuka; pakuti inu ndinu Yehova Mulungu wanga.

19Pakuti nditatembenuka, ndinalapa; nditalangizidwa, ndinamenya pa ntchafu yanga; ndinakhala ndi manyazi, inde, ndinapepulidwa, chifukwa ndinasenza chitonzo cha ubwana wanga.

20Yes. 63.15Kodi Efuremu ndiye mwana wanga wokondedwa? Kodi ndiye mwana wokondweretsa? Nthawi zonse zoti ndimnenera zomtsutsa, pakuti ndimkumbukiranso ndithu; chifukwa chake mumtima mwanga ndimlirira; ndidzamchitiradi chifundo, ati Yehova.

Aisraele adzakhalanso bwino m'dziko mwao

21Taimitsa zizindikiro, udzipangire zosonyeza; taika mtima wako kuyang'anira mseu wounda, njira imene unapitamo; tatembenukanso, iwe namwali wa Israele, tatembenukiranso kumizinda yako iyi.

22Udzayenda kwina ndi kwina masiku angati, iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo? Pakuti Yehova walenga chatsopano m'dziko lapansi: mkazi adzasanduka mphongo.

23Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Kawirinso adzanena mau awa m'dziko la Yuda ndi m'mizinda yake, pamene ndibwezanso undende wao; Yehova akudalitse iwe, wokhalamo chilungamo, iwe phiri lopatulika.

24Yer. 33.12-13Ndipo Yuda ndi mizinda yake yonse adzakhalamo pamodzi; alimi, ndi okusa zoweta.

25Pakuti ndakhutidwa mtima wolema, ndadzazanso mtima uliwonse wachisoni.

26Pamenepo ndinauka, ndinaona; ndipo tulo tanga tinandizunira ine.

27Taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzafesera nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda ndi mbeu ya anthu ndi mbeu ya nyama.

28Ndipo padzakhala kuti, monga ndayang'anira iwo kuzula ndi kupasula ndi kugwetsa, ndi kuononga ndi kusautsa; momwemo ndidzayang'anira iwo kumangitsa mudzi ndi kubzala, ati Yehova.

29Ezk. 18.2-3Masiku omwewo sadzanenanso, Atate adya mphesa zowawa, ndi mano a ana ayayamira.

30Agal. 6.5, 7Koma yense adzafa chifukwa cha mphulupulu yake; yense amene adya mphesa zowawa, mano ake adzayayamira.

Pangano latsopano pakati pa Mulungu ndi anthu ake

31 Ezk. 37.26; Aheb. 8.8-12 Taonani masiku adza, ati Yehova, ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israele, ndi nyumba ya Yuda;

32Ezk. 37.26; Aheb. 8.8-12si monga pangano limene ndinapangana ndi makolo ao tsiku lija ndinawagwira manja kuwatulutsa m'dziko la Ejipito; pangano langa limenelo analiswa, ngakhale ndinali mbuyao, ati Yehova.

33Ezk. 37.26; Aheb. 8.8-12Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israele atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika chilamulo changa m'kati mwao, ndipo m'mtima mwao ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, nadzakhala iwo anthu anga;

34Ezk. 37.26; Yoh. 6.45; Mac. 10.43; 1Ako. 2.10; Aheb. 8.8-12ndipo sadzaphunzitsa yense mnansi wake, ndi yense mbale wake, kuti, Mudziwe Yehova; pakuti iwo onse adzandidziwa, kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu wa iwo, ati Yehova; pakuti ndidzakhululukira mphulupulu yao, ndipo sindidzakumbukira tchimo lao.

35Gen. 1.16Yehova atero, amene apatsa dzuwa kuti liunikire usana, ndi malemba a mwezi ndi a nyenyezi kuti aunikire usiku, amene atonthoza nyanja, pamene mafunde ake agavira; Yehova wa makamu ndi dzina lake:

36Yes. 54.9Ngati malembawa achoka pamaso panga, ati Yehova, pamenepo mbeunso ya Israele idzaleka kukhala mtundu pamaso panga kunthawi zonse.

37Yer. 33.22Atero Yehova, Ngati ukhoza kuyesa thambo la kumwamba, ndi kusanthula pansi maziko a dziko, pamenepo ndidzachotsa mbeu zonse za Israele chifukwa cha zonse anazichita, ati Yehova.

38Neh. 3.1Taonani, masiku adza, ati Yehova, amene mzindawu udzamangidwira Yehova kuyambira pa Nsanja ya Hananele kufikira ku Chipata cha Kungodya.

39Ndipo chingwe choyesera chidzatulukanso kulunjika ku chitunda cha Garebu, ndipo chidzazungulira kunka ku Gowa.

40Neh. 3.28; Yow. 3.17Ndipo chigwa chonse cha mitembo, ndi cha phulusa, ndi minda yonse kufikira kumtsinje wa Kidroni, kufikira kungodya kwa Chipata cha Akavalo kuloza kum'mawa, ponsepo padzapatulikira Yehova; sipadzazulidwa, sipadzagwetsedwa konse kunthawi zamuyaya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help