1 Aleluya.
Lemekezani Yehova kochokera kumwamba;
mlemekezeni m'misanje.
2Mlemekezeni, angelo ake onse;
mlemekezeni, makamu ake onse.
3Mlemekezeni, dzuwa ndi mwezi;
mlemekezeni, nyenyezi zonse zounikira.
4 1Maf. 8.27 Mlemekezeni, m'mwambamwamba,
ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo.
5Alemekeze dzina la Yehova;
popeza analamulira, ndipo zinalengedwa.
6 Yer. 31.35-36 Anazikhazikanso kunthawi za nthawi;
anazipatsa chilamulo chosatumphika.
7Lemekezani Yehova kochokera ku dziko lapansi,
zinsomba inu, ndi malo ozama onse;
8moto ndi matalala, chipale chofewa ndi nkhungu;
mphepo ya namondwe, yakuchita mau ake;
9 Yes. 55.12 mapiri ndi zitunda zonse;
mitengo yazipatso ndi yamikungudza yonse:
10Nyama zakuthengo ndi zoweta zonse;
zokwawa, ndi mbalame zakuuluka.
11Mafumu a padziko ndi mitundu yonse ya anthu;
zinduna ndi oweruza onse a padziko.
12Anyamata ndiponso anamwali;
okalamba pamodzi ndi ana.
13 Yes. 12.4 Alemekeze dzina la Yehova;
pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka;
ulemerero wake uli pamwamba padziko lapansi ndi thambo.
14 Aef. 2.17 Ndipo anakweza nyanga ya anthu ake,
chilemekezo cha okondedwa ake onse;
ndiwo ana a Israele, anthu a pafupi pa Iye.
Aleluya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.