YESAYA 12 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Chiyamiko cha anthu a Mulungu atalangidwa

1Tsiku lomwelo udzati, Ndikuyamikani inu Yehova; pakuti ngakhale munandikwiyira, mkwiyo wanu wachoka, ndipo mutonthoza mtima wanga.

2Mas. 118.14Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.

3Yoh. 7.37-38Chifukwa chake mudzakondwera pakutunga madzi m'zitsime za chipulumutso.

4Mas. 148.13; Yoh. 17.1, 4, 6, 26Tsiku lomwelo mudzati, Muyamikire Yehova, bukitsani dzina lake, mulalikire machitidwe ake mwa mitundu ya anthu, munene kuti dzina lake lakwezedwa.

5Eks. 15.1Muimbire Yehova; pakuti wachita zaulemerero; chidziwike ichi m'dziko lonse.

6Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help