1 Agal. 1.11-12 Ndipo ndikudziwitsani, abale, Uthenga Wabwino umene ndinakulalikirani inu, umenenso munalandira, umenenso muimamo,
2Aro. 1.16umenenso mupulumutsidwa nao ngati muugwiritsa monga momwe ndinalalikira kwa inu; ngati simunakhulupirire chabe.
3Mas. 22; Yes. 53; Agal. 1.11-12Pakuti ndinapereka kwa inu poyamba, chimenenso ndinalandira, kuti Khristu anafera zoipa zathu, monga mwa malembo;
4Hos. 6.2; Luk. 24.26, 46ndi kuti anaikidwa; ndi kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu, monga mwa malembo;
5Luk. 24.34, 36ndi kuti anaonekera kwa Kefa; pamenepo kwa khumi ndi awiriwo;
6pomwepo anaoneka pa nthawi imodzi kwa abale oposa mazana asanu, amene ochuluka a iwo akhala kufikira tsopano, koma ena agona;
7Luk. 24.50pomwepo anaonekera kwa Yakobo; pamenepo kwa atumwi onse;
8Mac. 9.4, 17ndipo potsiriza pake pa onse, anaoneka kwa inenso monga mtayo.
9Mac. 8.3; Aef. 3.7-8Pakuti ine ndili wamng'ono wa atumwi, ndine wosayenera kutchedwa mtumwi, popeza ndinalondalonda Mpingo wa Mulungu.
10Aro. 15.18-19; 2Ako. 11.23Koma ndi chisomo cha Mulungu ndili ine amene ndili; ndipo chisomo chake cha kwa ine sichinakhale chopanda pake, koma ndinagwirira ntchito yochuluka ya iwo onse; koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine.
11Ngati ine tsono, kapena iwowa, kotero tilalikira, ndi kotero munakhulupirira.
12Koma ngati Khristu alalikidwa kuti waukitsidwa kwa akufa, nanga ena mwa inu anena bwanji kuti kulibe kuuka kwa akufa?
13Koma ngati kulibe kuuka kwa akufa, Khristunso sanaukitsidwe;
14ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe kulalikira kwathu kuli chabe, chikhulupiriro chanunso chili chabe.
15Mac. 2.24, 32Ndiponso ife tipezedwa mboni zonama za Mulungu; chifukwa tinachita umboni kunena za Mulungu kuti anaukitsa Khristu; amene sanamuukitse, ngati kuli tero kuti akufa saukitsidwa.
16Pakuti ngati akufa saukitsidwa, Khristunso sanaukitsidwe;
17Aro. 4.25ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe, chikhulupiriro chanu chili chopanda pake; muli chikhalire m'machimo anu.
18Chifukwa chake iwonso akugona mwa Khristu anatayika.
192Tim. 3.12Ngati tiyembekezera Khristu m'moyo uno wokha, tili ife aumphawi oposa a anthu onse.
20Akol. 1.18; 1Pet. 1.3Koma tsopano Khristu waukitsidwa kwa akufa, chipatso choyamba cha iwo akugona.
21Aro. 5.12, 17Pakuti monga imfa inadza mwa munthu, kuuka kwa akufa kunadzanso mwa munthu.
22Pakuti monga mwa Adamu onse amwalira, choteronso mwa Khristu onse akhalitsidwa ndi moyo.
23Koma yense m'dongosolo lake la iye yekha, chipatso choyamba Khristu; pomwepo iwo a Khristu, pakubwera kwake.
24Dan. 7.14, 27Pomwepo pali chimaliziro, pamene adzapereka ufumu kwa Mulungu, ndiye Atate, atatha kuthera chiweruzo chonse, ndi ulamuliro wonse, ndi mphamvu yomwe.
25Mas. 110.1Pakuti ayenera kuchita ufumu kufikira ataika adani onse pansi pa mapazi ake.
26Chiv. 20.14Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.
27Mas. 8.6Pakuti Iye anagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake. Koma pamene anena kuti zonse zagonjetsedwa, kuzindikirika kuti sawerengapo Iye amene anagonjetsa zonsezo kwa Iye.
281Ako. 3.23; 11.3Ndipo pamene zonsezo zagonjetsedwa kwa Iye, pomwepo Mwana yemwe adzagonjetsedwa kwa Iye amene anamgonjetsera zinthu zonse, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.
29Ngati si kutero, adzachita chiyani iwo amene abatizidwa chifukwa cha akufa? Ngati akufa saukitsidwa konse, abatizidwa chifukwa ninji chifukwa cha iwo?
302Ako. 11.26Nanga ifenso tili m'moopsa bwanji nthawi zonse?
31Aro. 8.36Ndifa tsiku ndi tsiku, ndilumbira pa kudzitamandira kwa inu, abale, kumene ndili nako mwa Khristu Yesu, Ambuye wathu.
32Yes. 22.13; 2Ako. 1.8Ngati ndinalimbana ndi zilombo ku Efeso monga mwa munthu, ndipindulanji? Ngati akufa saukitsidwa, tidye timwe pakuti mawa timwalira.
331Ako. 5.6Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.
34Aro. 13.11Ukani molungama, ndipo musachimwe; pakuti ena alibe chidziwitso cha Mulungu. Ndilankhula kunyaza inu.
35 Ezk. 37.3 Koma wina adzati, Akufa aukitsidwa bwanji? Ndipo adza nalo thupi lotani?
36Yoh. 12.24Wopusa iwe, chimene uchifesa wekha sichikhalitsidwanso chamoyo, ngati sichifa;
37ndipo chimene ufesa, sufesa thupi limene lidzakhala, koma mbeu yokha kapena ya tirigu kapena ya mtundu wina;
38koma Mulungu aipatsa thupi monga afuna; ndi kwa mbeu yonse thupi lakelake.
39Nyama yonse siili imodzimodzi; koma ina ndi ya anthu, ndi ina ndiyo nyama ya zoweta, ndi ina ndiyo nyama ya mbalame, ndi ina ya nsomba.
40Palinso matupi am'mwamba, ndi matupi apadziko: koma ulemerero wa lam'mwamba ndi wina, ndi ulemerero wa lapadziko ndi winanso.
41Kuli ulemerero wa dzuwa, ndi ulemerero wina wa mwezi, ndi ulemerero wina wa nyenyezi; pakuti nyenyezi isiyana ndi nyenyezi mu ulemerero.
42Mat. 13.43Chomwechonso kudzakhala kuuka kwa akufa. Lifesedwa m'chivundi, liukitsidwa m'chisavundi;
43Afi. 3.21lifesedwa m'mnyozo, liukitsidwa mu ulemerero; lifesedwa m'chifooko, liukitsidwa mumphamvu;
44lifesedwa thupi lachibadwidwe, liukitsidwa thupi lauzimu. Ngati pali thupi lachibadwidwe, palinso lauzimu.
45Gen. 2.7; Yoh. 5.21; Aro. 5.14Koteronso kwalembedwa, Munthu woyamba, Adamu, anakhala mzimu wamoyo. Adamu wotsirizayo anakhala mzimu wakulenga moyo.
46Koma chauzimu sichili choyamba, koma chachibadwidwe; pamenepo chauzimu.
47Yoh. 3.13, 31Munthu woyambayo ali wapansi, wanthaka. Munthu wachiwiri ali wakumwamba.
48Afi. 3.20-21Monga wanthakayo, ateronso anthaka; ndi monga wakumwamba, ateronso akumwamba.
49Gen. 5.3; Aro. 8.29Ndipo monga tavala fanizo la wanthakayo, tidzavalanso fanizo la wakumwambayo.
50 Yoh. 3.3, 5 Koma ndinena ichi, abale, kuti thupi ndi mwazi sizingathe kulowa Ufumu wa Mulungu; kapena chivundi sichilowa chisavundi.
511Ate. 4.15-17Taonani, ndikuuzani chinsinsi; sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika,
521Ate. 4.15-17m'kamphindi, m'kuthwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osavunda, ndipo ife tidzasandulika.
532Ako. 5.4Pakuti chovunda ichi chiyenera kuvala chisavundi, ndi chaimfa ichi kuvala chosafa.
54Yes. 25.8Ndipo pamene chovunda ichi chikadzavala chisavundi ndi chaimfa ichi chikadzavala chosafa, pamenepo padzachitika mau olembedwa, Imfayo yamezedwa m'chigonjetso.
55Hos. 13.14Imfawe, chigonjetso chako chili kuti? Imfawe, mbola yako ili kuti?
56Aro. 4.15Koma mbola ya imfa ndiyo uchimo; koma mphamvu ya uchimo ndiyo chilamulo:
57Aro. 7.25; 1Yoh. 5.4-5koma ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
582Pet. 3.14Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.