1 ATESALONIKA 2 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Za utumiki wake wa kwa Atesalonika

1Pakuti, abale, mudziwa nokha malowedwe athu a kwa inu, kuti sanakhale opanda pake;

2Mac. 16.22; 17.2-9koma tingakhale tidamva zowawa kale, ndipo anatichitira chipongwe, monga mudziwa, ku Filipi, tinalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m'kutsutsana kwambiri.

3Pakuti kudandaulira kwathu sikuchokera kukusochera, kapena kuchidetso, kapena m'chinyengo;

4Agal. 1.10; 1Tim. 1.11-12komatu monga Mulungu anativomereza kutiikiza Uthenga Wabwino, kotero tilankhula; osati monga okondweretsa anthu, koma Mulungu; amene ayesa mitima yathu.

52Ako. 2.17Pakuti sitinayende nao mau osyasyalika nthawi iliyonse monga mudziwa, kapena kupsinjika msiriro, mboni ndi Mulungu;

6Yoh. 5.41; 1Ako. 9.4, 6, 12, 18kapena sitinakhale ofuna ulemerero wa kwa anthu, kapena kwa inu, kapena kwa ena, tingakhale tinali nayo mphamvu yakukulemetsani monga atumwi a Khristu.

72Tim. 2.24Komatu tinakhala ofatsa pakati pa inu, monga m'mene mlezi afukata ana ake a iye yekha;

8Aro. 15.29; 2Ako. 12.15kotero ife poliralira inu, tinavomera mokondwera kupereka kwa inu si Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife.

9Mac. 20.34; 2Ako. 12.13-14Pakuti mukumbukira, abale, chigwiritso chathu ndi chivuto chathu; pochita usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu, tinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu.

102Ate. 3.7Inu ndinu mboni, Mulungunso, kuti tinakhala oyera mtima ndi olungama ndi osalakwa kwa inu akukhulupirira;

11monga mudziwa kuti tinachitira yense wa inu pa yekha, monga atate achitira ana ake a iye yekha,

12Aef. 4.1ndi kukudandaulirani, ndi kukusangalatsani ndi kuchita umboni, kuti muyende koyenera Mulungu, amene akuitanani inu mulowe ufumu wake wa Iye yekha, ndi ulemerero.

13 Mat. 10.40; 1Ate. 1.3 Ndipo mwa ichinso ife tiyamika Mulungu kosalekeza, kuti, pakulandira mau a Uthenga wa Mulungu, simunawalandire monga mau a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mau a Mulungu, amenenso achita mwa inu okhulupirira.

14Mac. 17.5, 13Pakuti inu, abale, munayamba kukhala akutsanza a Mipingo ya Mulungu yokhala mu Yudeya mwa Khristu Yesu; popeza zomwezi mudazimva kowawa ndinunso pamanja pa a mtundu wanu wa inu nokha, monganso iwowa pa manja a Ayuda;

15Mat. 23.34, 37; Mac. 3.15amene adaphanso Ambuye Yesu, ndi aneneri, natilondalonda ife, ndipo sakondweretsa Mulungu, natsutsana nao anthu onse;

16Mac. 17.5, 13natiletsa ife kuti tisalankhule ndi akunja kuti apulumutsidwe; kudzaza machimo ao nthawi zonse; koma mkwiyo wafika pa iwo kufikira chimaliziro.

Paulo alira kuonanso Atesalonika. Akondwera pa uthenga anabwera nao Timoteo

17 Akol. 2.5; 1Ate. 3.10 Koma ife, abale, angakhale adatichotsa kusiyana nanu kanthawi, osapenyana maso, koma kusiyana mtima ai, tinayesetsa koposa kuona nkhope yanu ndi chilakolako chachikulu;

18Aro. 1.13chifukwa tinafuna kudza kwa inu, inedi Paulo ndatero kamodzi kapena kawiri; koma Satana anatiletsa.

19Afi. 4.1Pakuti chiyembekezo chathu, kapena chimwemwe, kapena korona wakudzitamandira naye nchiyani? Si ndinu nanga, pamaso pa Ambuye wathu Yesu m'kufika kwake?

20Pakuti inu ndinu ulemerero wathu ndi chimwemwe chathu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help