1 Ower. 8.1-3; 1Sam. 25.10-13 Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo;
koma mau owawitsa aputa msunamo.
2Lilime la anzeru linena bwino zomwe adziwa;
koma m'kamwa mwa opusa mutsanulira utsiru.
3 Yer. 16.17; Aheb. 4.13 Maso a Yehova ali ponseponse,
nayang'anira oipa ndi abwino.
4Kuchiza lilime ndiko mtengo wa moyo;
koma likakhota liswa moyo.
5Chitsiru chipeputsa mwambo wa atate wake;
koma wosamalira chidzudzulo amachenjera.
6M'nyumba ya wolungama muli katundu wambiri;
koma m'phindu la woipa muli vuto.
7Milomo ya anzeru iwanditsa nzeru,
koma mtima wa opusa suli wolungama.
8 Yes. 1.11; Yer. 6.20 Nsembe ya oipa inyansa Yehova;
koma pemphero la oongoka mtima limkondweretsa.
9 1Tim. 6.11 Njira ya oipa inyansa Yehova;
koma akonda wolondola chilungamo.
10 1Maf. 22.8 Wosiya njira adzalangidwa mowawa;
wakuda chidzudzulo adzafa.
11 2Mbi. 6.30; Yoh. 2.24-25 Kumanda ndi kuchionongeko kuli pamaso pa Yehova;
koposa kotani nanga mitima ya ana a anthu?
12 2Tim. 4.3 Wonyoza sakonda kudzudzulidwa,
samapita kwa anzeru.
13 Miy. 17.22 Mtima wokondwa usekeretsa nkhope;
koma moyo umasweka ndi zowawa za m'mtima.
14Mtima wa wozindikira ufunitsa kudziwa;
koma m'kamwa mwa opusa mudya utsiru.
15Masiku onse a wosauka ali oipa;
koma wokondwera mtima ali ndi phwando losatha.
16 Mas. 37.16; 1Tim. 6.6 Zapang'ono, ulikuopa Yehova,
zipambana ndi katundu wambiri pokhala phokoso.
17 Miy. 17.1 Kudya masamba, pali chikondano,
kuposa ng'ombe yonenepa pali udani.
18Munthu wozaza aputa makani;
koma wosakwiya msanga atonthoza makangano.
19Mayendedwe a waulesi akunga linga laminga,
koma njira ya oongoka mtima iundidwa ngati mseu.
20Mwana wanzeru akondweretsa atate wake;
koma munthu wopusa apeputsa amake.
21 Aef. 5.15 Wosowa nzeru akondwera ndi utsiru;
koma munthu wozindikira aongola mayendedwe ake.
22Zolingalira zizimidwa popanda upo;
koma pochuluka aphungu zikhazikika.
23Munthu akondwera ndi mayankhidwe a m'kamwa mwake;
ndi mau a pa nthawi yake kodi sali abwino?
24 Afi. 3.20 Anzeru ayesa njira yamoyo yokwerakwera,
kuti apatuke kusiya kunsi kwa manda.
25 Mas. 68.5-6 Yehova adzapasula nyumba ya wonyada;
koma adzalembera mkazi wamasiye malire ake.
26Ziwembu zoipa zinyansa Yehova;
koma oyera mtima alankhula mau okondweretsa.
27 Yes. 5.8 Wopindula monyenga avuta nyumba yake;
koma wakuda mitulo adzakhala ndi moyo.
28 1Pet. 3.15 Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe;
koma m'kamwa mwa ochimwa mutsanulira zoipa.
29 Mas. 34.16; 145.18-19 Yehova atalikira oipa;
koma pemphero la olungama alimvera.
30Kuunika kwa maso kukondweretsa mtima;
ndipo pomveka zabwino mafupa amatenga uwisi.
31Khutu lomvera chidzudzulo cha moyo
lidzakhalabe mwa anzeru.
32Wokana mwambo apeputsa moyo wake;
koma wosamalira chidzudzulo amatenga nzeru.
33 Miy. 1.7 Kuopa Yehova ndiko mwambo wanzeru;
ndipo chifatso chitsogolera ulemu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.