NUMERI 32 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Arubeni, Agadi, ndi Amanase alandira cholowa chao tsidya lino la Yordani(Deut. 3.12-22)

1Koma ana a Rubeni ndi ana Gadi anali nazo zoweta zambirimbiri; ndipo anapenyerera dziko la Yazere, ndi dziko la Giliyadi, ndipo taonani, malowo ndiwo malo a zoweta.

2Pamenepo ana a Gadi ndi ana a Rubeni anadza nanena ndi Mose, ndi Eleazara wansembe, ndi akalonga a khamulo, nati,

3Ataroti, ndi Diboni, ndi Yazere, ndi Nimira, ndi Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Sibima, ndi Nebo, ndi Beoni,

4dzikoli Yehova analikantha pamaso pa gulu la Israele, ndilo dziko la zoweta ndipo anyamata anu ali nazo zoweta.

5Ndipo anati, Ngati tapeza ufulu pamaso panu, mupatse anyamata anu dziko ili likhale laolao; tisaoloke Yordani.

6Ndipo Mose anati kwa ana a Gadi ndi ana a Rubeni, Kodi abale anu apite kunkhondo, ndi inu mukhale pansi kuno?

7Ndipo mufoketseranji mtima wa ana a Israele kuti asaoloke ndi kulowa dzikoli Yehova anawapatsa?

8Num. 13.3Anatero makolo anu, muja ndinawatumiza achoke ku Kadesi-Baranea kukaona dziko.

9Popeza atakwera kunka ku chigwa cha Esikolo, naona dziko, anafoketsa mtima wa ana a Israele, kuti asalowe dzikoli Yehova adawapatsa.

10Ndipo Yehova anapsa mtima tsiku lija, nalumbira Iye, nati,

11Num. 14.24Anthu adakwerawo kutuluka mu Ejipito, kuyambira wa zaka makumi awiri ndi mphambu sadzaona dziko limene ndinalumbirira Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo; popeza sananditsate Ine ndi mtima wonse;

12Num. 14.24koma Kalebe mwana wa Yefune, Mkenizi, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo; popeza anatsata Yehova ndi mtima wonse.

13Ndipo Yehova anapsa mtima pa Israele, nawayendetsayendetsa m'chipululu zaka makumi anai, kufikira utatha mbadwo wonsewo udachita choipa pamaso pa Yehova.

14Ndipo taonani, mwauka m'malo mwa makolo anu, gulu la anthu ochimwa, kuonjezanso mkwiyo waukali wa Yehova pa Israele.

152Mbi. 7.19Pakuti mukabwerera m'mbuyo kusamtsata Iye, adzawasiyanso m'chipululu, ndipo mudzaononga anthu awa onse.

16Ndipo anayandikiza, nati Tidzamangira zoweta zathu makola kuno, ndi ana athu mizinda;

17koma ife tidzakhala okonzeka ndi kufulumira pamaso pa ana a Israele, kufikira tidawafikitsa kumalo kwao; ndi ang'ono athu adzakhala mizinda ya malinga chifukwa cha okhala m'dzikomo.

18Yos. 22.4Sitidzabwerera kwathu, kufikira ana a Israele atalandira yense cholowa chake.

19Pakuti sitidzalandira pamodzi nao tsidya la Yordani, ndi m'tsogolo mwake; popeza cholowa chathu tachilandira tsidya lino la Yordani kum'mawa.

20Ndipo Mose anati nao, Ngati mudzachita ichi, ndi kudzikonza kunkhondo pamaso pa Yehova,

21ndi kuoloka Yordani pamaso pa Yehova okonzeka onse mwa inu, kufikira atapirikitsa adani ake pamaso pake,

22ndi dziko lagonjera Yehova; mutatero mudzabwerere, ndi kukhala osachimwira Yehova ndi Israele; ndipo dziko ili lidzakhala lanulanu pamaso pa Yehova.

23Gen. 4.7; 44.16; Yes. 59.12Koma mukapanda kutero, taonani, mwachimwira Yehova; ndipo zindikirani kuti tchimo lanu lidzakupezani.

24Dzimangireni mizinda ya ana anu, ndi makola a zoweta zanu; ndipo muzichite zotuluka m'kamwa mwanu.

25Ndipo ana a Gadi ndi ana a Rubeni ananena ndi Mose, nati, Anyamata anu adzachita monga mbuyanga alamulira.

26Ana athu, akazi athu, zoweta zathu, ndi ng'ombe zathu zonse, zidzakhala komweko m'mizinda ya ku Giliyadi;

27Yos. 4.12koma anyamata anu adzaoloka, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova kunkhondo, monga wanena mbuyanga.

28Pamenepo Mose anamuuza Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a makolo a mafuko a ana a Israele za iwo.

29Ndipo Mose anati kwa iwo, Ngati ana a Gadi ndi ana a Rubeni aoloka nanu Yordani, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova, ndi dziko lagonjera inu; pamenepo muwapatse dziko la Giliyadi likhale laolao;

30koma akapanda kuoloka nanu okonzeka, akhale nao maiko aoao pakati pa inu m'dziko la Kanani.

31Ndipo ana a Gadi ndi ana a Rubeni anayankha, nati, Monga Yehova anati kwa anyamata anu momwemo tidzachita.

32Tidzaoloka okonzeka pamaso pa Yehova ku dziko la Kanani, koma cholowa chathuchathu chikhale tsidya lino la Yordani.

33Yos. 13.8Ndipo Mose anawapatsa, ndiwo ana a Gadi, ndi ana a Rubeni ndi hafu la fuko la Manase mwana wa Yosefe, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani, dzikoli ndi mizinda yake m'malire mwao, ndiyo mizinda ya dziko lozungulirako.

34Ndipo ana a Gadi anamanga Diboni, ndi Ataroti, ndi Aroere;

35Ataroti-Sofani, Yazere, ndi Yogobeha;

36ndi Betenimura, ndi Beteharani: mizinda ya m'malinga, ndi makola a zoweta.

37Ndipo ana a Rubeni anamanga Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Kiriyataimu;

38ndi Nebo, ndi Baala-Meoni (anasintha maina ao), ndi Sibima; ndipo anaitcha mizinda adaimanga ndi maina ena.

39Ndipo ana a Makiri mwana wa Manase ananka ku Giliyadi, naulanda, napirikitsa Aamori anali m'mwemo.

40Ndipo Mose anapatsa Makiri mwana wa Manase Giliyadi; ndipo anakhala m'menemo.

41Ndipo Yairi mwana wa Manase ananka nalanda midzi yao, naitcha Havoti-Yairi.

42Ndipo Noba ananka nalanda Kenati, ndi midzi yake, nautcha Noba, dzina lake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help