MASALIMO 16 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Munthu wokhulupirira Mulungu akhazikika mtima, osaopa kutayikaMikitamu wa Davide.

1 Mas. 25.20 Ndisungeni ine, Mulungu: pakuti ndakhulupirira Inu.

2Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Ambuye wanga,

ndilibe chabwino china choposa Inu.

3Za oyera mtima okhala padziko lapansi,

iwo ndiwo omveka mbiri,

mwa iwowo muli chikondwero changa chonse.

4Zidzachuluka zisoni zao za iwo otsata Mulungu wina.

Sindidzathira nsembe zao zamwazi,

ndipo sindidzatchula maina ao pakamwa panga.

5 Mas. 73.26; Mali. 3.24 Yehova ndiye gawo la cholowa changa ndi chikho changa,

ndinu wondigwirira cholandira changa.

6Zingwe zandigwera mondikondweretsa;

inde cholowa chokoma ndili nacho.

7 2Sam. 5.18-19 Ndidzadalitsa Yehova, amene anandichitira uphungu,

usikunso impso zanga zindilangiza.

8 Mac. 2.25-28 Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse;

popeza ali padzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.

9Chifukwa chake wasekera mtima wanga,

nukondwera ulemu wanga;

mnofu wanganso udzakhala mokhazikika.

10Pakuti simudzasiya moyo wanga kumanda;

simudzalola wokondedwa wanu avunde.

11 Mat. 5.8; 7.14; 1Ako. 13.12 Mudzandidziwitsa njira ya moyo,

pankhope panu pali chimwemwe chokwanira;

m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help