MIYAMBO 11 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 Deut. 25.13-16 Muyeso wonyenga unyansa Yehova;

koma mulingo wamphumphu umsekeretsa.

2 Dan. 4.30-31 Pakudza kudzikuza padzanso manyazi;

koma nzeru ili ndi odzichepetsa.

3Kuongoka mtima kwa olungama kuwatsogolera;

koma kukhota kwa achiwembu kudzawaononga.

4 Gen. 7.1; Ezk. 7.19 Chuma sichithandiza tsiku la mkwiyo;

koma chilungamo chipulumutsa kuimfa.

5Chilungamo cha wangwiro chimaongola njira yake;

koma woipa adzagwa ndi zoipa zake.

6 Mlal. 10.8 Chilungamo cha oongoka mtima chidzawapulumutsa;

koma achiwembu adzagwidwa ndi mphulupulu yao.

7Pomwalira woipa chidikiro chake chionongeka;

chiyembekezo cha uchimo chionongeka.

8Wolungama apulumuka kuvuto;

woipa nalowa m'malo mwake.

9 Yob. 8.13 Wonyoza Mulungu aononga mnzake ndi m'kamwa mwake;

koma olungama adzapulumuka pakudziwa.

10Olungama akapeza bwino, mzinda usekera;

nufuula pakuonongeka oipa.

11Madalitso a olungama akuza mzinda;

koma m'kamwa mwa oipa muupasula.

12 Lev. 19.16 Wopeputsa mnzake asowa nzeru;

koma wozindikira amatonthola.

13Kazitape woyendayenda amawanditsa zinsinsi;

koma wokhulupirika mtima abisa mau.

14 1Maf. 12.1-19 Popanda upo wanzeru anthu amagwa;

koma pochuluka aphungu pali chipulumutso.

15Woperekera mlendo chikole adzaphwetekwapo;

koma wakuda chikole akhala ndi mtendere.

16 Miy. 31.30 Mkazi wodekha agwiritsa ulemu;

aukali nagwiritsa chuma.

17 Mat. 5.7 Wachifundo achitira moyo wake zokoma;

koma wankhanza avuta nyama yake.

18 Hos. 10.12 Woipa alandira malipiro onyenga;

koma wofesa chilungamo aonadi mphotho.

19Wolimbikira chilungamo alandira moyo;

koma wolondola zoipa adzipha yekha.

20Okhota mtima anyansa Yehova;

koma angwiro m'njira zao amsekeretsa.

21 Mas. 112.2 Zoonadi, wochimwa sadzapulumuka chilango;

koma mbeu ya olungama idzalanditsidwa.

22Monga chipini chagolide m'mphuno ya nkhumba,

momwemo mkazi wokongola wosasinkhasinkha bwino.

23Chifuniro cha olungama chifikitsa zabwino zokha;

koma chiyembekezo cha oipa mkwiyo.

24 Mas. 112.9 Alipo wogawira, nangolemerabe;

aliponso womana chomwe ayenera kupatsa nangosauka.

25 2Ako. 9.6-9 Mtima wa mataya udzalemera;

wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.

26 Amo. 8.4-6 Womana tirigu anthu amtemberera;

koma madalitso adzakhala pamutu pa wogulitsa.

27Wopwaira ubwino afunitsa chikondwerero;

koma zoipa zidzamfikira wozilondola.

28 Yer. 17.8; Mrk. 10.24 Wokhulupirira chuma chake adzagwa;

koma olungama adzaphuka ngati tsamba.

29Wovuta banja lake adzalowa m'zomsautsa;

wopusa adzatumikira wanzeru.

30 Dan. 12.3; 1Ako. 9.19-23; Yak. 5.20 Chipatso cha wolungama ndi mtengo wa moyo;

ndipo wokola mtima ali wanzeru.

31 Yer. 25.29; 1Pet. 4.17-18 Taonani, wolungama adzalandira mphotho kunja kuno;

koposa kotani woipa ndi wochimwa?

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help