1 Gen. 29.32-35 Ana a Israele ndi awa: Rubeni, Simeoni, Levi, ndi Yuda, Isakara, ndi Zebuloni,
2Gen. 30.24; 35.18Dani, Yosefe, ndi Benjamini, Nafutali, Gadi, ndi Asere.
3Ana a Yuda ndiwo Eri, ndi Onani, ndi Sela; Batisuwa Mkanani anambalira atatu amenewa. Koma Eri mwana woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova, ndi Iye anamupha.
4Ndi Tamara mpongozi wake anambalira Perezi ndi Zera. Ana aamuna onse a Yuda ndiwo asanu.
5Ana a Perezi: Hezironi, ndi Hamuli.
6Ndi ana a Zera: Zimiri, ndi Etani, ndi Hemani, ndi Kalikoli, ndi Dara; onse pamodzi ndi asanu.
7Yos. 7.1Ndi ana a Karimi: Akara wovuta Israeleyo, amene analakwira choperekedwa chiperekerecho.
8Ndi mwana wa Etani: Azariya.
9Ndi ana a Hezironi anambadwirawo: Yerameele, ndi Ramu, ndi Kalebe.
10Ndi Ramu anabala Aminadabu; ndi Aminadabu anabala Nasoni kalonga wa ana a Yuda;
11Rut. 4.21ndi Nasoni anabala Salimoni, ndi Salimoni anabala Bowazi,
12ndi Bowazi anabala Obedi, ndi Obedi anabala Yese,
13ndi Yese anabala mwana wake wamwamuna woyamba Eliyabu, ndi Abinadabu wachiwiri, ndi Simea wachitatu,
14Netanele wachinai, Radai wachisanu,
151Sam. 16.13Ozemu wachisanu ndi chimodzi, Davide wachisanu ndi chiwiri;
162Sam. 2.18ndi alongo ao ndiwo Zeruya ndi Abigaile. Ndi ana a Zeruya: Abisai ndi Yowabu, ndi Asahele; atatu.
17Ndi Abigaile anabala Amasa; ndi atate wa Amasa ndiye Yetere Mwismaele.
18Ndi Kalebe mwana wa Hezironi anabala ana ndi Azuba mkazi wake, ndi Yerioti; ndipo ana ake ndiwo Yesere, ndi Sobabu, ndi Aridoni.
19Namwalira Azuba, ndi Kalebe anadzitengera Efurata, amene anambalira Huri.
20Ndi Huri anabala Uri, ndi Uri anabala Bezalele.
21Ndipo pambuyo pake Hezironi analowa kwa mwana wamkazi wa Makiri atate wa Giliyadi, amene anamtenga akhale mkazi wake, pokhala wa zaka makumi asanu ndi limodzi mwamunayo; ndipo mkaziyo anambalira Segubu.
22Ndi Segubu anabala Yairi, amene anali nayo mizinda makumi awiri mphambu itatu m'dziko la Giliyadi.
23Ndi Gesuri ndi Aramu analanda mizinda ya Yairi, pamodzi ndi Kenati ndi midzi yake; ndiyo mizinda makumi asanu ndi limodzi. Iwo onse ndiwo ana a Makiri atate wa Giliyadi.
24Ndipo atafa Hezironi mu Kalebe-Efurata, Abiya mkazi wa Hezironi anambalira Asiriya atate wa Tekowa.
25Ndi ana a Yerameele mwana woyamba wa Hezironi ndiwo: woyamba Ramu, ndi Buna, ndi Oreni, ndi Ozemu, ndi Ahiya.
26Ndipo Yerameele anali naye mkazi wina dzina lake ndiye Atara, ndiye make wa Onamu.
27Ndipo ana a Ramu mwana woyamba wa Yerameele ndiwo Maazi, ndi Yamini, ndi Ekeri.
28Ndi ana a Onamu ndiwo Samai, ndi Yada; ndi ana a Samai: Nadabu, ndi Abisuri.
29Ndipo dzina la mkazi wa Abisuri ndiye Abihaili; ndipo anambalira Abani, ndi Molidi.
30Ndi ana a Nadabu: Seledi ndi Apaimu; koma Seledi anamwalira wopanda ana.
31Ndi mwana wa Apaimu: Isi. Ndi mwana wa Isi: Sesani. Ndi mwana wa Sesani: Alai.
32Ndi ana a Yada mbale wa Samai: Yetere, ndi Yonatani; namwalira Yetere wopanda ana.
33Ndi ana a Yonatani: Peleti, ndi Zaza. Ndiwo ana a Yerameele.
34Ndipo Sesani analibe ana aamuna, koma ana aakazi. Ndi Sesani anali naye mnyamata Mwejipito dzina lake ndiye Yara.
35Ndipo Sesani anampatsa Yara mnyamata wake mwana wake wamkazi akhale mkazi wake, ndipo anambalira Atai.
36Ndipo Atai anabala Natani, ndi Natani anabala Zabadi,
37ndi Zabadi anabala Efilala, ndi Efilala anabala Obedi,
38ndi Obedi anabala Yehu, ndi Yehu anabala Azariya,
39ndi Azariya anabala Helezi, ndi Helezi anabala Eleasa,
40ndi Eleasa anabala Sisimai, ndi Sisimai anabala Salumu,
41ndi Salumu anabala Yekamiya, ndi Yekamiya anabala Elisama.
42Ndi ana a Kalebe mbale wa Yerameele ndiwo Mesa mwana wake woyamba, ndiye atate wa Zifi; ndi ana a Maresa atate wa Hebroni.
43Ndi ana a Hebroni: Kora, ndi Tapuwa, ndi Rekemu, ndi Sema.
44Ndi Sema anabala Rahama atate wa Yorikeamu, ndi Rekemu anabala Samai.
45Ndi mwana wa Samai ndiye Maoni; ndipo Maoni ndiye atate wa Betezuri.
46Ndi Efa mkazi wamng'ono wa Kalebe anabala Harani, ndi Moza, ndi Gazezi; ndi Harani anabala Gazezi.
47Ndi ana a Yadai: Regemu, ndi Yotamu, ndi Gesani, ndi Peleti, ndi Efa, ndi Saafi.
48Maaka mkazi wamng'ono wa Kalebe anabala Sebere, ndi Tirihana.
49Yos. 15.17Iyeyu anabalanso Saafi atate wa Madimana, Seva atate wa Makibena, ndi atate wa Gibea; ndi mwana wamkazi wa Kalebe ndiye Akisa.
50Ana a Kalebe ndi awa: mwana wa Huri, mwana woyamba wa Efurata, Sobala atate wa Kiriyati-Yearimu.
51Salima atate wa Betelehemu, Harefi atate wa Betegadere.
52Ndipo Sobala atate wa Kiriyati-Yearimu anali ndi ana: Harowe, ndi Hazi Amenuwoti.
53Ndi mabanja a Kiriyati-Yearimu: Aitiri, ndi Aputi, ndi Asumati, ndi Amisrai; Azorati ndi Aestaoli anafuma kwa iwowa.
54Ana a Salima: Betelehemu, ndi Anetofa, Ataroti-Beti-Yowabu, ndi Hazi Amanahati, ndi Azori.
55Ower. 1.16; 2Maf. 10.15; Yer. 35.2Ndi mabanja a alembi okhala ku Yabezi: Atirati, Asimeati, Asukati. Iwo ndiwo Akeni ofuma ku Hamati, kholo la nyumba ya Rekabu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.