1A magawidwe a odikira a Akora: Meselemiya mwana wa Kore wa ana a Asafu.
2Ndipo Meselemiya anali ndi ana, woyamba Zekariya, wachiwiri Yediyaele, wachitatu Zebadiya, wachinai Yatiniele,
3wachisanu Elamu, wachisanu ndi chimodzi Yehohanani, wachisanu ndi chiwiri Eliehoenai.
4Ndipo Obededomu anali nao ana, woyamba Semaya, wachiwiri Yehozabadi, wachitatu Yowa, wachinai Sakara, wachisanu Netanele,
5wachisanu ndi chimodzi Amiyele, wachisanu ndi chiwiri Isakara, wachisanu ndi chitatu Peuletai; pakuti Mulungu adamdalitsa.
6Kwa Semaya mwana wake yemwe kunabadwa ana, akulamulira nyumba ya atate wao; pakuti anali ngwazi zamphamvu.
7Ana a Semaya: Otini, ndi Refaele, ndi Obedi, Elizabadi, amene abale ao ndiwo odziwa mphamvu, Elihu, ndi Semakiya.
8Onsewa ndiwo a ana a Obededomu; iwo ndi ana ao, ndi abale ao, anthu odziwa mphamvu yakutumikira, makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri a Obededomu.
9Ndi Meselemiya anali ndi ana, ndi abale odziwa mphamvu khumi mphambu asanu ndi atatu.
10Hosa yemwe wa ana a Merari anali ndi ana, wamkulu ndi Simiri; pakuti ngakhale sanali wobadwa woyamba, atate wake anamuyesa wamkulu;
11wachiwiri Hilikiya, wachitatu Tebaliya, wachinai Zekariya; ana ndi abale onse a Hosa ndiwo khumi ndi atatu.
12Mwa iwowa munali magawidwe a odikira, mwa akulu a amuna akuchita udikiro wao, monga abale ao, kutumikira m'nyumba ya Yehova.
131Mbi. 25.8Ndipo anachita maere, ang'ono ndi akulu, monga mwa nyumba za makolo ao, kuchitira zipata zonse.
14Ndi maere a kum'mawa anagwera Selemiya. Ndipo anachitira maere Zekariya mwana wake, phungu wanzeru, ndi maere anamgwera kumpoto;
15Obededomu kumwera, ndi ana ake nyumba ya akatundu.
16Supimu ndi Hosa kumadzulo, ku chipata cha Saleketi, ku mseu wokwerapo, udikiro pandunji pa udikiro.
17Kum'mawa kunali Alevi asanu ndi mmodzi, kumpoto anai tsiku ndi tsiku, kumwera anai tsiku ndi tsiku, ndi a nyumba ya akatundu awiri ndi awiri.
18Ku Parabara kumadzulo anai kumseu, ndi awiri ku Parabara.
19Awa ndi magawidwe a odikira; a ana a Akora, ndi a ana a Merari.
Osunga chuma Nyumba ya Mulungu20 Mala. 3.10 Ndipo wa Alevi, Ahiya anayang'anira chuma cha nyumba ya Mulungu, ndi chuma cha zopatulika.
21Ana a Ladani: ana a Ladani a Ageresoni, akulu a nyumba za makolo a Ladani Mgeresoni, Yehiyeli.
22Ana a Yehiyeli: Zetamu ndi Yowele mbale wake, oyang'anira chuma cha nyumba ya Yehova.
23Aamuramu, Aizihara, Ahebroni, Auziyele;
24ndi Sebuele mwana wa Geresomo, mwana wa Mose, ndiye mkulu woyang'anira zuma.
25Ndi abale ake a Eliyezere: Rehabiya mwana wake, ndi Yesaya mwana wake ndi Yoramu mwana wake, ndi Zikiri mwana wake, ndi Selomoti mwana wake.
26Selomoti amene ndi abale ake anayang'anira chuma chonse cha zinthu zopatulika, zimene Davide mfumu ndi akulu a nyumba za akulu, akulu a zikwi ndi mazana, adazipatula.
27Kutenga pa zofunkha kunkhondo, anapatulako kukonzera nyumba ya Yehova.
28Ndipo zonse adazipatula Samuele mlauli, ndi Saulo mwana wa Kisi, ndi Abinere mwana wa Nere, ndi Yowabu mwana wa Zeruya; aliyense anapatula kanthu kalikonse, anazisunga Selomoti ndi abale ake.
Akapitao ndi oweruza29A Aizihara: Kenaniya ndi ana ake anachita ntchito ya pabwalo ya Israele, akapitao ndi oweruza milandu.
30A Ahebroni: Hasabiya ndi abale ake odziwa mphamvu chikwi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri anayang'anira Israele tsidya lino la Yordani kumadzulo, kuyang'anira ntchito yonse ya Yehova, ndi kutumikira mfumu.
31Yeriya ndiye mkulu wa Ahebroni, wa Ahebroni monga mwa mibadwo ya nyumba za makolo. Chaka cha makumi anai cha ufumu wa Davide anafunafuna, napeza mwa iwowa ngwazi zamphamvu ku Yazere wa ku Giliyadi.
322Mbi. 19.11Ndi abale ake ngwazi ndiwo zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri, akulu a nyumba za makolo, amene mfumu Davide anaika akhale oyang'anira a Arubeni, ndi Agadi, ndi hafu la fuko la Manase, pa zinthu zonse za Mulungu ndi zinthu za mfumu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.